Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 27 tsamba 174-tsamba 178 ndime 3
  • Kulankhula Kuchokera mu Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Kuchokera mu Mtima
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula Kochokera m’Maganizo ndi Kulankhula Mwadzidzidzi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kugwiritsa Ntchito Autilaini
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kukonza Autilaini
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 27 tsamba 174-tsamba 178 ndime 3

PHUNZIRO 27

Kulankhula Kuchokera mu Mtima

Kodi muyenera kuchita motani?

Lankhulani m’njira yotchula mawu mwachibadwa ndi mfundo zokonzekera mosamala.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Kulankhula kuchokera mu mtima ndiyo njira yoposa yokopera chidwi cha omvera ndi kuwalimbikitsa.

MUKHOZA kuyesetsa mwakhama kukonza nkhani yanu. Mukhozanso kusanja mfundo zothandiza kwambiri. Nkhaninso yotsatirika bwino. Ndi kuikamba mosadodoma. Koma ngati maganizo a omvera anu sali okhazikika—ngati akungotolapo zina mwa zimene mukunena chifukwa maganizo awo akumapita ku zinthu zina—kodi nkhani yanu ingawathandize? Ngati akulephera kutchera khutu ku nkhani yanu, kodi n’zotheka kuti muwafike pamtima?

Kodi chingachititse vuto limenelo n’chiyani? Zifukwa zilipo zosiyanasiyana. Koma kaŵirikaŵiri kumakhala kulephera kulankhula nkhani kuchokera mu mtima. Kunena kwina, wokamba nkhaniyo amakhala akuyang’ana pamanotsi pafupipafupi kwambiri, kapena sakulankhula mwachibadwa. Komanso, mavuto ameneŵa amakhalaponso chifukwa cha mmene munthu wakonzekerera nkhani yake.

Ngati muyamba ndi kulemba nkhani yanu yonse kenako n’kuisintha kukhala autilaini, mudzapeza kuti n’kovuta kukamba nkhaniyo mochokera mu mtima. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwasankha kale mawu enieni amene mukufuna kukawalankhula. Ngakhale kuti mugwiritse ntchito autilaini pokamba nkhaniyo, mudzakhala mukuyesabe kukumbukira mawu amene munawalemba pankhani yoyamba ija. Nkhani ikalembedwa, mawu ake sakhala achibadwa ndipo masentensi ake amakhala ovutirapo kusiyana ndi kalankhulidwe ka masiku onse. Zimenezi zimaonekera pamene mukukamba nkhani.

M’malo molemba mawu onse a nkhani yanu, yesani zotsatirazi: (1) Sankhani mutu wa nkhani ndi mfundo zake zazikulu zimene mudzafotokoza potambasula mutuwo. Ngati ili nkhani yaifupi, mfundo ziŵiri zokha zingakhale zokwanira. Nkhani yaikulu ingakhale ndi mfundo zinayi kapena zisanu basi. (2) Pansi pa mfundo yaikulu iliyonse, lembani malemba ofunika kwambiri amene mukufuna kukaŵerenga potambasula nkhaniyo; lembaninso mafanizo ndi zifukwa zanu. (3) Ganiziraninso mmene mudzayambire nkhaniyo. Mukhoza kulemba sentensi imodzi kapena aŵiri. Konzaninso mawu omaliza.

Kukonzekera kakambidwe ka nkhani n’kofunika kwambiri. Koma musapende liwu ndi liwu la nkhaniyo ndi cholinga chakuti muiloŵeze yonse pamtima. Pokonzekera nkhani yolankhula kuchokera mu mtima, ikani mtima makamaka pa mfundo zimene muzikafotokoza, osati mawu. Muyenera kuzisinkhasinkha mobwerezabwereza mfundozo kufikira zitalumikizana bwinobwino m’maganizo mwanu. Ngati nkhani yanu mwaiyala m’ndondomeko yotsatirika ndipo mwaikonzekeranso bwino, mbali imeneyi siingakhalenso yovuta ayi; pokambanso nkhani yanu, mfundozo zimangobwera mwachibadwa ndi mosavuta.

Ganizirani Mapindu Ake. Ubwino waukulu wa kukamba nkhani kuchokera mu mtima ndi wakuti muzilankhula monga mwa masiku onse. Ndiko kulankhula kumene anthu amalabadira msanga. Kakambidwe kanu kazikhala kaumoyo ndi kosangalatsa kwa omvera anu.

Kakambidwe kameneka kamakupatsani mpata wokwanira woyang’ana omvera, kumene kumakuthandizani kuyendera nawo limodzi. Chifukwa simukudalira manotsi anu potchula sentensi iliyonse, omvera anu adzaona kuti nkhani yanu mukuidziŵa bwino ndipo mukukhulupiriradi zimene mukunena. Motero, kakambidwe kotero kamachititsa nkhani kukhala yochokera pansi pa mtima, yokhala ngati kukambirana, ndi yowafika pamtima omvera.

Kukamba nkhani kuchokera mu mtima kumalolanso kusinthasintha. Mfundozo sizikhala zoti simungathe kusintha mbali zina. Tiyerekeze kuti m’maŵa wa tsiku lanu lokamba nkhaniyo, pamveka nkhani ina panyuzi yokhudza kwambiri anthu yogwirizana ndi nkhani yanuyo. Kodi sikungakhale koyenera kuiloŵetsapo? Kapena tinene kuti pamene mukukamba nkhani, mukuona kuti pakati pa omvera anu pali ana ambiri a misinkhu yopita kusukulu. N’kulekeranji kusintha zitsanzo zanu ndi tanthauzo lake kuti muthandize anawo kumvetsa mmene nkhaniyo ikukhudzira miyoyo yawo!

Ubwino wina wa kakambidwe kochokera mu mtima ndi wakuti kamalimbikitsa maganizo anu. Pamene muli patsogolo pa omvera oyamikira ndi olabadira, amakupatsani mphamvu ndipo mumayesetsa kumveketsa bwino mfundo zanu, ngakhalenso kubwereza mfundo zina kuti zikhomerezeke. Mukaona kuti chidwi cha omvera chikuzirala, mumayesetsa kuchitapo kanthu kuti mukopenso maganizo awo kusiyana ndi kungolankhula kwa anthu amene maganizo awo ali kwina.

Peŵani Mbuna. Dziŵaninso kuti kulankhula kochokera mu mtima kulinso ndi mbuna zake. Imodzi mwa mbunazo ndi kudya nthaŵi. Ngati pokamba nkhani yanu muloŵetsapo mfundo zambiri zowonjezera, nthaŵi ikuvutani. Mungapeŵe zimenezi mwa kulemba nthaŵi pa gawo lililonse la autilaini yanu. Mukatero tsatirani kwambiri nthaŵi zimenezo.

Mbuna ina, makamaka kwa okamba nkhani ozoloŵera, ndi kudzidalira kwambiri. Pokhala ozoloŵera kukamba pamaso pa anthu ambiri, ena angaone kuti n’kosavuta kusonkhanitsa mfundo zingapo msangamsanga ndi kukazikamba m’nthaŵi yoperekedwayo. Koma kudzichepetsa ndi kuzindikira mfundo yakuti tikusamalira gawo limene tangopatsidwako m’pulogalamu yophunzitsa imene Yehova mwini wakeyo ndiye Mlangizi Wamkulu, kudzatithandiza kusamalira nkhani iliyonse mwa pemphero ndi kuikonzekera bwino.—Yes. 30:20; Aroma 12:6-8.

Mwina nkhaŵa yaikulu kwa osazoloŵera kukamba nkhani kuchokera mu mtima ndi yakuti angaiŵale zimene anafuna kunena. Musalole nkhaŵa imeneyi kukuletsani kupita patsogolo pa luso la kulankhula limeneli. Konzekerani bwino, ndipo pemphani chithandizo cha Yehova cha mzimu wake woyera.—Yoh. 14:26.

Anthu ena safuna kukamba nkhani kuchokera mu mtima poopa kulakwitsa mawu. N’zoonadi kuti pokamba nkhani kuchokera mu mtima simungathe kutchula mawu osankhidwa bwino kwambiri ndipo simungatsatire galamala mofanana ndi nkhani yoŵerenga, koma chimene chimakhala bwino kwambiri koposa zimenezo n’chakuti mumalankhula m’njira yokhala ngati kukambirana. Anthu amalabadira mosavuta ngati mfundo zikambidwa m’mawu osavuta kumva komanso m’kalankhulidwe ka masiku onse. Ngati mukonzekera bwino, mawu oyenerera adzangofika mwachibadwa, osati chifukwa mwawaloŵeza pamtima ayi, koma chifukwa mfundozo munazikonzekera mokwanira. Komanso ngati m’kulankhula kwanu kwa masiku onse mumalankhula mawu oyenerera, kudzangochitika mwachibadwa pamene muli pa pulatifomu.

Mtundu wa Manotsi Amene Muyenera Kugwiritsa Ntchito. M’kupita kwa nthaŵi komanso mwa kuzoloŵera, mungamalembe autilaini ya mawu ochepa chabe pa mfundo iliyonse ya nkhani yanu. Mawu ochepawo, limodzi ndi malemba amene mufuna kugwiritsa ntchito, mungawalembe pa khadi kapena kapepala kuti muzitha kukumbukira msanga. Pokonzekera utumiki wa kumunda, nthaŵi zambiri mudzangofunikira kuloŵeza ka autilaini kosavuta. Ngati munafufuza nkhani yokakambirana paulendo wobwereza, mungalembe manotsi achidule pa kapepala ndi kukaphatika m’Baibulo lanu. Kapena mungagwiritse ntchito autilaini yochokera pa “Nkhani Zokambirana za m’Baibulo” kapena mfundo zochokera m’buku lakuti Kukambitsirana za m’Malemba, monga maziko a makambirano anu.

Komabe, ngati mwapatsidwa magawo osiyanasiyana pamsonkhano m’milungu yochepa chabe, mwinanso kuphatikizapo nkhani za onse, mungafunikire manotsi ochulukirapo. Chifukwa chiyani? Kuti mukathe kubwereramonso m’mfundo za nkhani iliyonse musanaikambe. Ngakhale ndi choncho, ngati mudalira kwambiri manotsi pokamba nkhani yanu—ngati muyang’anapo pofuna kutchula sentensi iliyonse—mudzataya mapindu a kukamba nkhani kuchokera mu mtima. Ngati mugwiritsa ntchito manotsi ochulukirapo, chongani kapena lembani mizera pansi pa mawu angapo kapena malemba a m’nkhani yanu amene mukufuna kuŵerenga.

Ngakhale kuti nkhani yokambidwa ndi munthu wozoloŵera kwakukulukulu iyenera kukambidwa kuchokera mu mtima, pangakhalenso mapindu ena ngati aphatikizaponso njira zina zokambira nkhani. M’mawu oyamba ndi mawu omaliza, mmene kuyang’ana omvera kuyenera kuyendera limodzi ndi mawu amphamvu osankhidwa bwino, kungakhale kothandiza kukhalapo ndi masentensi angapo amene mwawaloŵeza pamtima. Ngati mukatchula zochitika, ziŵerengero, mawu ogwidwa, kapena mawu a m’malemba, kuchita kuziŵerenga kumakhala bwino ndipo kumagwira mtima kwambiri.

Pamene Ena Afunsa Chifukwa. Nthaŵi zina, pamene sitinakonzekere, anthu ena angatifunse kuti tipereke zifukwa pankhani zokhudza chikhulupiriro chathu. Zimenezi zingachitike pamene munthu wina m’munda atsutsa nkhani ina. Zoterozo zingachitikenso pamene tili ndi achibale, anzathu kuntchito, kapena kusukulu. Akuluakulu a boma angafunenso kuti tipereke zifukwa pankhani zokhudza chikhulupiriro chathu ndi moyo wathu. Malemba amatilangiza kuti: “[Khalani] okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.”—1 Pet. 3:15.

Taonani mmene Petro ndi Yohane anayankhira Khoti Lalikulu la Ayuda pa Machitidwe 4:19, 20. M’masentensi aŵiri okha, iwo anamveketsa bwino lomwe mbali imene anaimako. Anachita zimenezo m’njira yoyenera malinga ndi anthu amene anali kulankhula nawo—ndipo anaonetsa kuti nkhani imene inali pamaso pawo inalinso pamaso pa khotilo. Pambuyo pake, Stefano anaimbidwa milandu yongom’namizira, ndipo anapita naye ku khoti limodzimodzilo. Ŵerengani zifukwa zake zosayembekezera koma zamphamvu pa Machitidwe 7:2-53. Kodi mfundo zake anazisanja motani? Anafotokoza tsatanetsatane wa mbiri ya zochitika. Panthaŵi yoyenerera, anayamba kutsindika za mzimu wa chipanduko umene mtundu wa Israyeli unaonetsa. Pomalizira pake, anasonyeza kuti Khoti Lalikulu la Ayudalo linasonyeza mzimu wofananawo mwa kulamula imfa ya Mwana wa Mulungu.

Ngati mwafunsidwa mosayembekezera kuti mupereke zifukwa pankhani yokhudza chikhulupiriro chanu, n’chiyani chingakuthandizeni kulankhula mawu ogwira mtima? Tengerani chitsanzo cha Nehemiya, amene anapemphera mu mtima asanayankhe funso lochokera kwa Mfumu Aritasasta. (Neh. 2:4) Mukatero, msangamsanga konzani autilaini ya m’maganizo. Mungatsatire masitepe ofunikira aŵa: (1) Sankhani mfundo imodzi kapena ziŵiri zimene mukufuna kufotokoza (mfundozo zingakhale zimene zimapezeka m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba) (2) Sankhani malemba amene mukufuna kugwiritsa ntchito ngati maziko a mfundo zanu. (3) Konzani mmene muyambire nkhani yanu mosamala kuti wofunsayo akhale ndi chidwi chomvetsera. Pamenepo yambani kulankhula.

Kodi mukadzapanikizidwa mudzakumbukira zoyenera kuchita? Yesu anauza otsatira ake kuti: “Musamadera nkhaŵa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthaŵi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.” (Mat. 10:19, 20) Izi sizikutanthauza kuti mudzalankhula “mawu a nzeru” mwa njira ya chozizwitsa, muja zinachitikira kwa Akristu a m’zaka 100 zoyambirira ayi. (1 Akor. 12:8) Koma ngati mumatengera mwayi nthaŵi zonse maphunziro amene Yehova amapereka kwa atumiki ake mu mpingo wachikristu, mzimu woyera udzakukumbutsani mfundo zofunikazo panthaŵi yake.—Yes. 50:4.

Kunena zoona, kukamba nkhani kuchokera mu mtima kungakhale kogwira mtima kwambiri. Ngati muyesetsa kutero pokamba nkhani zanu mu mpingo, ndiye kuti muzitha kuyankha mosavuta mafunso osawayembekezera, chifukwa masitepe ake ndi ofanana. Musazengereze. Kuphunzira kulankhula kuchokera mu mtima kudzakuthandizani kupangitsa utumiki wanu wa kumunda kukhala wogwira mtima kwambiri. Ndipo ngati muli ndi mwayi wokamba nkhani mu mpingo, muzitha kukopa chidwi cha omvera ndi kuwafika pamtima.

MMENE MUNGAPEZERE LUSOLO

  • Kumbukirani mapindu a kukamba nkhani kuchokera mu mtima.

  • M’malo molemba nkhani yanu yonse, konzani autilaini yosavuta.

  • Konzekerani nkhani yanu mwa kupenda mfundo iliyonse payokha mu mtima. M’malo modera nkhaŵa kwambiri za mawu, samalani kwambiri za kufotokoza mfundo m’ndondomeko yotsatirika.

ZOCHITA: (1) Pokonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, onetsetsani kuti mukuchonga kapena kulemba mizera kunsi kwa mawu ofunika okhawo m’malo mwa masentensi onse. Yankhani m’mawu anu. (2) Pokonzekera nkhani yanu yotsatira mu sukulu, yambani mwa kutchula kuchokera mu mtima mutu wa nkhani komanso mfundo zazikulu ziŵiri kapena zitatu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena