Lalikirani Mwaluntha
1 Kuti tikhale ndi luntha tifunikira kuzindikira kanthu kena ponena za anthu amene timawalalikira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kukhoza kwathu kufikira mitima ya anthu kumadalira pa luso lathu la kupereka uthenga wa Ufumu m’njira imene imawakopa. Mkati mwa mwezi wa January, tidzagaŵira mabuku osiyanasiyana ophunzirira Baibulo amene mpingo ungakhale nawo. Koma, makamaka ofalitsa adzagaŵira buku la Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? Malingaliro otsatirawa angakhale othandiza.
2 Ngati musankha kugaŵira buku la “Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?” mungasonyeze chithunzithunzi cha patsamba 4 ndi kunena kuti:
◼ “Chithunzithunzichi chili lingaliro la wojambula pa zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi. Kodi nchiyani chimene mukuganiza kuti chifunikira kuti inu ndi banja lanu mudzakhale m’dziko lapansi laparadaiso? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limasonyeza kuti mtendere weniweni ndi chisungiko zidzakhalapodi padziko lonse lapansi posachedwa ndi kuti Paradaiso adzabwezeretsedwa. [Ŵerengani Salmo 37:10, 11.] Buku ili lingakusonyezeni zimene muyenera kuchita kuti mudzapindule ndi zimene Mulungu adzachita. Ndikufuna kukusiyirani bukuli.”
3 Pamene mukugaŵira buku la “Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe” munganene zonga izi:
◼ “Kodi mungavomereze kuti banja lamakono likuyang’anizana ndi mavuto amene anali osadziŵika ndi anthu kumbuyoku? [Yembekezerani yankho.] Mwa kulingalira kwanu, kodi nchifukwa ninji zimenezi zikuchitika? [Yamikirani yankho lake. Tsegulani ndi kuŵerenga 2 Timoteo 3:1-3.] Mawu akuti ‘osamvera akuwabala’ ndi akuti ‘opanda chikondi chachibadwidwe’ amalongosola molondola za anthu ambiri m’tsiku lathu. Komabe, Mulungu mmodzimodziyo amene ananeneratu za mavuto ameneŵa watipatsanso chitsogozo chanzeru cha mmene tingachititsire banja kukhala logwirizana kwambiri.” Ŵerengani ndime ya “Afalitsi” patsamba 2. Yembekezerani ndemanga, gaŵirani bukulo.
4 Kafikidwe kena kamene kangagwiritsiridwe ntchito pa buku lakuti “Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?,” ndi koyamba ndi funso ili:
◼ “Lerolino anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu alibe chidwi chenicheni mwa anthufe padziko lapansi pano ndi kuti sadzachita chilichonse pamavuto amene alipo. Kodi mumalingalira choncho? [Yembekezerani yankho.] Imani ndikuŵerengereni zimene buku lothandiza kuphunzira Baibulo ili limanena ponena za cholinga cha Mulungu kulinga kwa anthu ndi dziko lapansi. [Ŵerengani ndime 1 ndi chiganizo choyamba m’ndime 2 patsamba 43.] Ndithudi, pali chifukwa chabwino chimene Mulungu walekerera mavuto omwe ali padziko lapansi. Ngati mukufuna kuchidziŵa, chonde ŵerengani buku ili, lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?” Ngati munthuyo ayamikira chidziŵitsocho, m’gaŵireni bukulo.
5 Ngati mukufuna kupereka ulaliki wachidule mogwiritsira ntchito buku la “Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa ‘Kalonga wa Mtendere,”’ mungatsegule bukulo patsamba 4 ndi kufunsa kuti:
◼ “Kodi pulaneti la Dziko Lapansi lidzakhala lotani? Ambiri amafuna kudziŵa zimenezi. Kodi muganiza kuti lingadzakhale paradaiso?” Yamikirani yankho la mwini nyumba, ndiyeno ŵerengani mawu oyamba a patsamba 2. Gaŵirani bukulo.
6 Luntha labwino lidzatikhozetsa kuzindikira zosoŵa ndi zinthu zokondweretsa anthu amene timakumana nawo. Miyambo 16:23 imatitsimikiziritsa zimenezi, ikumati: “Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake, nuphunzitsanso milomo yake.”