Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/06 tsamba 7
  • Anasonyeza Chitsanzo cha Kukhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anasonyeza Chitsanzo cha Kukhulupirika
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Madalitso a Utumiki wa Upainiya
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Chikumbutso kwa Mlembi ndi Woyang’anira Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Limbikirani Muutumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 7/06 tsamba 7

Anasonyeza Chitsanzo cha Kukhulupirika

1 Ntchito yatsopano ya utumiki wa nthawi zonse inayamba m’chaka cha 1937. Ndipo ntchitoyi ndi upainiya wapadera. Amuna ndi akazi amene akanakwanitsa, ndiponso odziwa bwino utumiki wachikristu, anavomera mwa kufuna kwawo kukatumikira kulikonse kumene gulu la Yehova linawatumiza. Tsopano, pambuyo pazaka zambiri, apainiya apadera akupitirizabe kupereka chitsanzo cha kukhulupirika chimene ndi chofunika kuchitsanzira.—Aheb. 6:12.

2 Anatsogolera Ntchito Yolalikira: Poyamba, apainiya apadera ankatsogolera ntchito yolalikira pogwiritsa ntchito galamafoni zing’onozing’ono pakhomo la mwini nyumba. Pamaulendo obwereza ankagwiritsanso ntchito galamafonizi kukambira nkhani za m’Baibulo. Zimenezi zinkachitika m’mizinda ikuluikulu mmene munali mutakhazikitsidwa kale mipingo. Kenako, apainiya apadera ankatumizidwa ku malo komwe olengeza ufumu ankafunika ambiri. Anapitirizabe kubwerera kwa anthu onse omwe asonyeza chidwi ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Chifukwa cha khama lawo, mipingo yambiri inapangidwa. Ntchito yawo yolalikira uthenga wabwino imene anagwira mosatopa, inachititsa kuti gulu la Yehova liwonjezeke kwambiri monga mmene tikulionera masiku ano. (Yes. 60:22) Apainiya apadera akupitiriza kuchita mbali yaikulu polengeza uthenga wabwino ku “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”—Akol. 1:23.

3 N’ngoyenera Kuwatsanzira: Apainiya ena apadera akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambiri. Chikhulupiriro cha amuna ndi akazi okhulupirika amenewa chayengeka chifukwa cha zinthu zambiri zimene akumana nazo pamoyo wawo. (1 Pet. 1:6, 7) Iwo akhala ndi mtima wofuna kutaya chuma chawo n’cholinga chokatumikira ku malo kumene kuli zosowa zapadera. Ena tsopano akalamba ndipo amadwaladwala, kapena amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (2 Akor. 4:16, 17) Komabe akupitiriza ‘kupatsa zipatso [ngakhale kuti] akalamba.’ (Sal. 92:14) Amakhulupirira Yehova ndipo amalandira madalitso ake.—Sal. 34:8; Miy. 10:22.

4 Zoonadi, tiyenera kuwayamikira kwambiri apainiya apadera. Ngati muli ndi mwayi wokhala ndi apainiya apadera mumpingo mwanu, pezeranipo mwayi wocheza nawo ndi kupindula kuchokera ku zimene anthu amenewa amakumana nazo. Sonyezani kuti mumayamikira utumiki wawo wolengeza Ufumu mokhulupirika. Tsanzirani kulimba mtima kwawo. Onse amene amatsanzira chikhulupiriro chawo, Yehova amawayanja ndi kuwadalitsa. Zili choncho chifukwa chakuti Iye amasangalala ndi anthu onse amene amachita zinthu mokhulupirika.—Miy. 12:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena