Kodi Mumanyalanyaza?
Kunyalanyaza chiyani? Kulemba khadi la DPA (Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala) limene Mboni zobatizidwa zimafunika kukhala nalo. Palibe ‘amene amadziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.’ Choncho, m’pofunika kusankhiratu chithandizo chamankhwala chimene mungalandire patachitika ngozi ndi kulemba zimene mwasankhazo. (Yak. 4:14; Mac. 15:28, 29) Pofuna kukuthandizani pankhani imeneyi, tikukupemphani kuti muonenso zimene zili mu mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2005. Tengani khadi lanu la DPA ndi kutsagana ndi wokamba nkhaniyi pokambirana mafunso awa:
(1) Pamfundo 1, kodi muyenera kulembapo chiyani? (2) (a) Tchulani zinthu ziwiri zimene mumatsimikizira monga wa Mboni za Yehova pamfundo 2. (b) Kodi chifukwa chachikulu chimene timakanira kuikidwa magazi n’chiyani? (3) (a) Kodi mfundo 3 ikufotokoza za chiyani? (b) Popanga zosankha, kodi tiyenera kuchita chiyani? (c) Mogwirizana ndi malemba awa, Aroma 14:12 ndi Agalatiya 6:5, kodi chinthu chofunika kuchiganizira popanga zosankha n’chiyani? (d) N’chifukwa chiyani m’pofunika kutsatira chikumbumtima chophunzitsidwa bwino? (e) Pambuyo poganizira mwapemphero za nkhaniyi, kodi muyenera kulemba chiyani pamadanga omwe ali pa khadiyi? (f) Kodi zimatanthauza chiyani mukalemba zilembo zoimira mayina anu pa danga la pa “(a) Ndikukana zonse (b) Ndikukana zonse kupatulapo:”? (g) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati pa mfundo 3 palibe zimene mwasankha? (4) (a) Kodi mfundo 4 ikunena za chiyani? (b) Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene muyenera kuwerenga ndi kuziganizira mwapemphero popanga zosankha? (c) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati pa mfundo 4 palibe zimene mwasankha? (5) (a) Kodi mfundo 5 ikunena za chiyani? (b) Kodi muyenera kuwerenga magazini iti popanga zosankha pankhani imeneyi? (c) Kenako, potsatira chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo, kodi muyenera kulemba pati zilembo zoimira mayina anu? (d) Ngati mungafune kufotokoza zambiri, kodi mungalembe pati? (6) (a) Kodi mukuyenera kuchita chiyani pamfundo 6? (b) Kodi muyenera kulemba mayina, maadiresi ndi manambala a foni za ndani pa madanga amenewa? (c) Kodi muyenera kulembera kuti khadi la DPA? (d) Ngakhale kuti munthu angalembere ku nyumba khadili, kodi payenera kukhala mboni zingati posainira khadili?
Kodi mwasankha chithandizo chamankhwala chenicheni chimene inu ndi ana anu mungalandire? Kuti muwerenge nkhani zimenezi mwatsatanetsatane, onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, ndi October 15, 2000 ndiponso nkhani yakuti “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala,” m’mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006. Zinthu zimene mwasankhazo muyenera kudziwitsa anthu okuimirani pa chithandizo chamankhwala ndiponso achibale anu onse omwe si Mboni.