Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 8/8 tsamba 5-11
  • Mungakhale ndi Moyo Wautali Komanso Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungakhale ndi Moyo Wautali Komanso Wabwino
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa Zotsekereza Zimenezi
  • Zizoloŵezi Zimene Zimakhudza Moyo Wanu
  • Chinanso Ndi Malo Amene Mukukhala
  • Alipo—Mankhwala Otsika Mtengo Koma Ochiritsiratu
  • Njira Yatsopano Yolimbana ndi Chifuwa cha TB
    Galamukani!—1999
  • Chipambano ndi Tsoka
    Galamukani!—1998
  • Kuithetsa Padziko Lonse Kodi Nkotheka?
    Galamukani!—1998
  • Anthu Akuona Ukalamba Mosiyana ndi Kale
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 8/8 tsamba 5-11

Mungakhale ndi Moyo Wautali Komanso Wabwino

TANGOYEREKEZANI kuti moyo wa munthu ndi liŵiro la mpikisano lamtunda wautali—liŵiro limene othamanga ayenera kudumpha zinthu zowatsekereza njira. Othamanga onse akuyambira liŵirolo pamodzi, koma podumphapo nthaŵi zina akumagunda zowatsekereza njirazo, ndipo othamangawo akufooka, ndipo ambiri akusiya kuthamanga.

Mofananamo, moyo wa munthu uli ndi poyambira komanso zotsekereza zitalizitali m’njira yake. M’moyo wake munthu amadumpha zotsekereza zimenezi nthaŵi ndi nthaŵi. Nthaŵi iliyonse imene wadumpha chotsekereza amafooka, ndipo m’kupita kwa nthaŵi iye amatopa. Ngati zotsekereza njira zimenezi zili zitalizitali, ndiye kutinso amatopa msanga, kapena amafa. Ngati munthuyo amakhala m’dziko lotukuka, amatopa akafika zaka 75. Nthaŵi imeneyi imatchedwa kuti utali umene anthu ambiri amatha kukhala ndi moyo—ndipo tingaiyerekezere ndi mtunda umene othamanga ambiri angathamange.a (Yerekezerani ndi Salmo 90:10.) Komabe, anthu ena amathamanga mtunda wautalipo, ndipo ochepa chabe mwa iwo amatha kufika pa malekezero pa utali umene anthu amatha kukhala ndi moyo, umene amati mwina ndi zaka 115 kapena mpaka 120—liŵiro losachitikachitika limene ngati litamalizidwa lingamveke padziko lonse.

Kudziŵa Zotsekereza Zimenezi

Tsopano, anthu akutha kuthamanga kwa nthaŵi yoŵirikiza kaŵiri tikayerekezera ndi kuchiyambi kwa zaka za zana lino. Chikuwatheketsa kutero n’chiyani? Chifukwa chachikulu n’chakuti munthu wakwanitsa kufupikitsa zotsekereza njira. Koma kodi zotsekereza njira zimenezi ndi chiyani? Ndipo kodi zingathe kufupikitsidwa kuposa pamenepa?

Katswiri wa zathanzi la anthu wa m’bungwe la World Health Organization (WHO) analongosola kuti zina mwa zotsekereza njira zimenezi, kapena kungoti zinthu, zimene zimakhudza moyo umene munthu amayembekezereka kukhala, ndizo chizoloŵezi chake, malo ake okhala, ndi chisamaliro cha zachipatala.b Motero ngati muli ndi zizoloŵezi zabwino, ndiye kuti malo anu okhala amakhala aukhondo, potero ndiye kuti chisamaliro cha zachipatala chikhalanso chabwinopo, pameneponso ndiye kuti zokutsekerezani njira zija zafupika, ndiye kutinso moyo wanu ukhala wautali mowonjezereka. Ngakhale kuti mikhalidwe ya anthu imasiyana kwambiri, pafupifupi aliyense—kongoyambira mkulu woyang’anira banki ku Sydney mpaka munthu wogulitsa zinthu m’misewu ya ku São Paulo—angachitepo kanthu kuti afupikitse zotsekereza njira zimenezi m’moyo wawo. Kodi angatero motani?

Zizoloŵezi Zimene Zimakhudza Moyo Wanu

“Anthu amene ali ndi zizoloŵezi zabwino amakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali, komanso samafa ziwalo msanga mpaka ku mapeto enieni a moyo,” ikutero magazini ya zachipatala yotchedwa The New England Journal of Medicine. N’zoonadi kuti chotsekereza choyamba chingathe kufupikitsidwa posintha zizoloŵezi monga madyedwe, kumwa, kugona, kusuta, ndi maseŵera olimbitsa thupi. Mwachitsanzo, tiyeni tionepo za zizoloŵezi zokhudza ntchito zolimbitsa thupi.

Maseŵera olimbitsa thupi. Kuchita maseŵera olimbitsa thupi mosapambanitsa kungakupindulitseni kwambiri. (Onani bokosi lakuti “Utali ndi Mtundu wa Maseŵera Olimbitsa Thupi Ukhale Wotani?”) Kufufuza kwasonyeza kuti maseŵera olimbitsa thupi osavuta ochitidwa m’nyumba komanso panja pa nyumba amathandiza okalamba, ngakhale ‘okalamba a okalamba,’ kuti akhalenso ndi nyonga komanso moyo wamphamvu. Mwachitsanzo, gulu lina la anthu achikulire a zaka zapakati pa 72 ndi 98 anaona kuti ankatha kuyenda mwamsangako komanso ankatha kukwera masitepe mosavuta pambuyo pochita maseŵera onyamula zitsulo zolemera kwa masabata khumi okha basi. Ndipotu izi n’zosadabwitsa! Atayesedwa pambuyo pa nthaŵi imeneyi anapeza kuti mphamvu za m’minofu yawo tsopano zinawonjezereka moŵirikiza kuposa kale. Gulu lina limene ambiri anali amayi ongokhala a zaka zofika 70, linali kuchita maseŵera olimbitsa thupi kaŵiri pamlungu. Patatha chaka chimodzi, kunapezeka kuti minofu yawo yawonjezereka kulemera, ndiponso mphamvu ndi kulinganizika, ndiponso mafupa awo anali olimbirapo. Katswiri wina wa maphunziro a ziwalo zam’thupi dzina lake Mirriam Nelson, ndiye amene anachita kafukufuku ameneyu, ndipo anati: “Pamene tinayamba, tinali kuchita mantha kuti mwina iwo adzayamba kubinya ndiponso kudzipweteka mafupa kapenanso minofu, koma potsiriza tinapeza kuti zinawachititsa kuti akhale amphamvu ndi a thanzi labwinopo.”

Ponena mwachidule zotsatirapo za kufufuza kosiyanasiyana kokhudza ukalamba ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi, buku lina linanena kuti: “Kulimbitsa thupi kumachedwetsa ukalamba, kumawonjezera moyo, ndipo kumachepetsa kudza kwa nyengo yodalira ena imene nthaŵi zambiri mapeto ake amakhala imfa.”

Zizoloŵezi zokhwimitsa maganizo. Mawu a kale akuti “uchigwiritse ntchito apo ayi chichita dzimbiri” akuoneka kuti samatanthauza thupi lokha komanso maganizo. Ngakhale kuti ukalamba umachititsanso kuiwalaiwala zinthu zina, kufufuza kochitidwa ndi bungwe lotchedwa U.S. National Institute on Aging kukuonetsa kuti ubongo wa okalamba umakhala wamphamvu zokwanira kuthana nazo zotsatirapo za ukalamba. Motero polofesa wina wa ubongo, Dr. Antonio R. Damasio, anati: “Anthu achikulire angathe kukhalabe ndi moyo wamaganizo abwinobwino ndiponso olongosoka.” Kodi chimachititsa kuti ubongo wa anthu achikulire uzikhalabe wogwira ntchito bwino ndi chiyani?

Ubongo uli ndi maselo okwana 100 biliyoni amene amatchedwanso kuti manyuroni, ndipo amakhala olumikizidwalumikizidwa kokwanira ka thiriliyoni. Kulumikizana kumeneku kuli ngati mawaya a telefoni ndipo kumatheketsa kuti maselo a m’bongo ameneŵa otchedwa manyuroni “aziyankhulitsana” ndi kuti azitha kukumbukira zinthu, komanso kuti azitha kuchita zinthu zina. Ubongo ukamakalamba, manyuroni amafa. (Onani bokosi lakuti “Maselo a Muubongo Awonedwa Mwatsopano”) Komabe ubongo wachikulire umatha kubwezeretsa manyuroni amene umataya. Nthaŵi iliyonse nyuroni ina ikafa, manyuroni oyandikana nayo amadzilumikiza ndi manyuroni ena motero amapitiriza ntchito imene nyuroni yatayikayo yasiya. Mwa njira imeneyi, ubongo umasintha ntchito yochitidwa ndi mbali yake ina kuipititsa kuti ikachitidwe kumbali ina. Choncho, anthu ambiri achikulire amachita ntchito zambiri zimene anthu achinyamata amachita, koma mwina amagwiritsira ntchito mbali zosiyana za ubongo kuti azichite. Tinganene kuti, ubongo wachikulire umakhala ngati munthu wachikulire woseŵera maseŵera a tennis amene chifukwa chakuti sangathe kuthamanga kwambiri amagwiritsa ntchito maluso ena amene oseŵera ena achinyamata mwina alibe. Komabe, ngakhale kuti amagwiritsa ntchito maluso osiyana ndi amene achinyamatawo amagwiritsa ntchito, woseŵera wachikulireyo amagoletsabe zigoli.

Kodi anthu achikulire angatani kuti azigoletsa zigoli zofanana ndi za anzawowo? Atachita kafukufuku mwa anthu 1,000 a zaka zapakati pa 70 ndi 80, katswiri wina wa zamaphunziro a zaukalamba Dr. Marilyn Albert anapeza kuti kukhwimitsa maganizo ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimachititsa kuti anthu achikulire ena akhalebe anzeru zochuluka. (Onani bokosi lakuti “Kufeŵetsa Maganizo Anu.”) Kulimbitsa maganizo kumachititsa kuti ‘mawaya a telefoni’ a mu ubongo azigwirabe ntchito. Koma, akatswiri akuti pamene “anthu asiya kugwira ntchito n’kumangokhala phwi, n’kumati alibe nako ntchito kusintha kwa dziko, zotsatirapo zake ndizo kusiya kugwira ntchito bwino kwa ubongo.”—Buku lotchedwa Inside the Brain (Mkati mwa Ubongo)

Motero, nkhani yabwino ndi yakuti “zinthu zimene zingathe kutithandiza kuti tikalambe bwino tingathe kuzilamulira kapena kuzisintha,” akulongosola motero Dr. Jack Rowe. Ndiponso, si kuti panopo mwachedwa kwambiri kwakuti simungathe kuyamba zizoloŵezi zabwino. Wofufuza wina ananena kuti: “Ngakhale ngati kale munali ndi zizoloŵezi zowononga thanzi lanu, zochita zanu komanso inuyo mumasintha kwambiri m’zaka zanu zaukalamba, muyenerabe kukolola ena mwa mapindu a moyo wosawononga thanzi.”

Chinanso Ndi Malo Amene Mukukhala

Ngati mwana wamkazi amene wabadwa lero ku London atatumizidwa ku London wakale kwambiri wa m’Nyengo Zapakati, utali wa moyo umene angayembekezereke kukhala ungakhale theka chabe la umene angayembekezereke kukhala tsopano. Chimene chingachititse zimenezi si kusintha kwa thupi la mwanayo ayi, koma mmalo mwake ndi kusintha kwakukulu kwa zotsekereza njira zinanso ziŵiri—Malo okhala ndi chisamaliro cha zachipatala. Poyamba, tiyeni tione kaye malo okhala.

Malo okuzungulirani. Kale, malo omuzungulira munthu—mwachitsanzo, mudzi wake—anali oopsa kwambiri kuthanzi. Komabe, m’zaka makumi angapo zapita posachedwazi zoopsa zimene zinali kuchititsidwa ndi malo ozungulira munthu zachepetsedwa. Tsopano thanzi la munthu ndi labwinopo ndipo moyo wakenso wawonjezeka chifukwa chakuti malo omuzungulira akonzedwa ndiponso ndi aukhondo, madzi abwino, ndi kuchepa kwa tizilombo tosautsa tam’nyumba. Ndipo zotsatirapo zake n’zakuti, m’malo ambiri a padziko lapansi, munthu akutha kuthamanga mtunda wautalipo.c Komabe, kufupikitsa chotsekereza njira chimenechi si kuti ndi kungokhala ndi chimbudzi chogejemula m’nyumba kokha ayi. Komanso n’kofunika kukhala bwino ndi anthu a kumene mukukhala ndiponso anthu amene mumapembedza nawo.

Anthu a kumene mukukhala. Kumene mukukhala kuli anthu—amene mumakhala nawo, kugwira nawo ntchito, kudya nawo, kulambira nawo, ndi kuseŵera nawo. Malo okuzungulirani amasamalika ngati muli ndi madzi abwino; chimodzimodzinso ndi anthu amene mukukhala nawo; iwo amakhala othandiza, ngati ena ali anzanu amene mumakondana nawo kwambiri, kungotchulapo chifukwa chimodzi chabe. Kutha kusangalala ndi kuchita chisoni pamodzi ndi ena, kuuzana zolakalaka zanu komanso zokhumudwitsa, kumafupikitsa chotsekereza njira chija ndipo kumakuthandizani kuthamanga mtunda wautalipo.

Koma, ngati si choncho ndiye kuti zinthu zichitika mosiyana. Kupanda anzanu kungachititse kusungulumwa ndiponso kudzipatula kwa anthu. Sukhala wosangalala ngati anthu amene ukukhala nawo sasonyeza kuti amaona kuti ndiwe wofunika. Mayi wina amene anali kukhala kunyumba zosungirako anthu okalamba analemba kuti: “Ndine wa zaka 82 ndipo ndakhala kunyumba kuno kwa zaka 16 zathunthu. Amatisunga bwino, koma kungoti nthaŵi zina kumakhala kovuta kupirira nako kusungulumwa.” N’zomvetsa chisoni kuti zimene akuona mayi ameneyu ndi zimene anthu ambiri achikulire akuona makamaka m’mayiko a azungu. Nthaŵi zambiri anthu a kumene amakhala amawalola kuti akhale nawo koma saona kufunika kwawo. Choncho, “kusungulumwa ndiko vuto limodzi limene limachititsa kuti anthu achikulire a kumayiko otukuka asamakhale bwino,” akutero James Calleja, wa m’bungwe loona za anthu okalamba padziko lonse lotchedwa International Institute on Ageing.

N’zoona kuti simungathe kuchotsa mikhalidwe imene imakuchititsani inu kusungulumwa—mikhalidwe monga kupuma pa ntchito nthaŵi imene simukufuna, kuvutika poyenda ndi kusiyana ndi anthu amene akhala anzanu kwa nthaŵi yaitali, kapenanso imfa ya mkazi kapena mwamuna wanu—komabe mungachitepo zinthu zina kuti mufupikitse chotsekereza chimenechi kuchiika pa utali woti mungathe kuchidumpha. Kwa amene mwangoyamba kumene, dziŵani kuti kusungulumwa sikuchititsidwa ndi ukalamba ayi; achinyamata ena nawo amasungulumwa. Kukalamba sikumene kwachititsa vutolo ayi—koma ndi kupatulidwa ku anthu. Kodi mungachite chiyani kuti mupeŵe kukhala opatulidwa.

“Dzichititseni kuti anthu azisangalala akakhala nanu,” akulangiza motero mayi wina wachikulire amene ali wamasiye. “Anthu ambiri sakonda kukhala ndi munthu wokonda kudandaula. Muyenera kuyesetsa kuti mukhale a nsangala. N’zoona kuti zimenezi zimafunika khama koma khama limeneli limapindulitsa pambuyo pake. Chifundo chimabala chifundo.” Anawonjeza kuti: “Ndimayesetsa kuŵerenga nyuzi ndiponso kumvetsera nkhani kotero kuti ndizikhala ndi nkhani zimene ndingathe kukambirana ndi anthu amene ndimakumana nawo, achinyamata kapenanso achikulire.”

Malingaliro ena nawa: Phunzirani kuchita chidwi ndi zinthu zimene anthu ena amakonda. Funsani mafunso. Yesetsani kukhala oolowa manja mmene mungathere. Ngati mulibe zinthu zoti mungathe kugawira ena, mungathe kupereka mphamvu zanu; muli chimwemwe m’kupatsa. Lembani makalata. Pezani chinthu chokusangalatsani choti muzichita nthaŵi yopuma. Lolani kuyendera anthu ena pamene akuitanani kapena kupita nawo kwinakwake kokasangalala. Nyumba yanu ikhale yachimwemwe ndipo yosangalatsa kwa alendo. Apezeni anthu amene ali ofuna chithandizo ndipo athandizeni.

Chipembedzo chanu kumene mukukhalako. Umboni ukuchulukira, wakuti zochitika za chipembedzo zimathandiza anthu achikulire kuona kuti “ali ndi tanthauzo ndi ofunika m’moyo” ndiponso kukhala ndi “chimwemwe”, “komanso kudzimva kukhala ofunika,” “kukhutira kwambiri ndi moyo,” “ndiponso kudzimva kuti ali mbali ya anthu onse komanso kuti ali ndi thanzi labwino.” N’chifukwa chiyani zili choncho? Buku lakuti Later Life—The Realities of Aging (Moyo Wauchikulire—Zoona Zake za Ukalamba) likulongosola kuti: “Chikhulupiriro cha chipembedzo chimapatsa anthu lingaliro linalake la moyo komanso kaonedwe ka zinthu, miyezo, ndi zikhulupiriro zimene zimawathandiza kuti amvetse ndiponso kuti azindikire zinthu zimene zikuchitika.” Kuphatikizanso apo pazochitika za chipembedzo anthu achikulire amakumana ndi anthu ena motero “sapatulidwa kwambiri ndi anthu ena ndiponso sasungulumwa.”

Kwa Louise ndi Evelyn, amene ali amayi amasiye a zaka 80 mumpingo wina wa Mboni za Yehova, nkhani zino zikungotsimikizira zimene akhala akudziŵa kwa zaka zambiri. “Ku Nyumba yathu ya Ufumu,d ndimasangalala kwambiri poyankhula ndi ena, achikulire ndi achinyamata omwe,” akutero Louise.“Misonkhano imakhala yophunzitsa. Misonkhano ikatha timasekanso kwambiri tikamacheza kuti tizidziŵana. Ndi nthaŵi yosangalatsa.” Evelyn nayenso amapindula ndi zimene amachita kopembedza. “Kukayankhulitsana ndi anthu nkhani za Baibulo, kumandichititsa kuti ndisadzipatule ku anthu. Koma chofunika kwambiri n’chakuti kumandichititsa kukhala wosangalala. Ntchito yothandiza ena kudziŵa tanthauzo lenileni la moyo ndi yokhutiritsa.”

Mwachionekere, Louise ndi Evelyn ali ndi cholinga m’moyo. N’chifukwa chake amakhala athanzi, motero amafupikitsa chotsekereza chachiŵiri—malo owazungulira—ndipo motero amapitirizabe liŵirolo.—Yerekezerani ndi Salmo 92:13, 14.

Alipo—Mankhwala Otsika Mtengo Koma Ochiritsiratu

Kupita patsogolo kwa sayansi ya zachipatala m’zaka za zana lino kwafupikitsa chotsekereza chachitatu; chisamaliro cha zachipatala, mofulumira kwambiri—koma osati padziko lonse. Lipoti lonena za thanzi la anthu padziko lotchedwa The World Health Report 1998, linati “m’mayiko angapo amene akutukuka kumene, utali wa moyo umene munthu amayembekezereka kukhala unatsika pakati pa 1975 ndi 1995.” Mkulu wa bungwe la WHO anati anthu atatu mwa anthu anayi alionse m’mayiko amene akutukuka kumene tsopano amafa asanafike zaka 50—umene unali utali wa moyo umene anthu akhala akuyembekezereka kukhala m’zaka zokwana theka la zana zapitazi.”

Ngakhalebe zinthu zili choncho, anthu ochulukirabe achikulire ndi achinyamata omwe m’mayiko amene akutukuka kumene akufupikitsa chotsekereza chimenechi pogwiritsa ntchito chisamaliro cha zachipatala chimene chilipo ndiponso chimene angathe kuchikwanitsa. Mwachitsanzo, pali njira yatsopano yochizira chifuwa cha TB.

Padziko lonse TB imapha anthu ambiri kuposa AIDS, malungo, ndi matenda onse a kumadera otentha—anthu 8,000 patsiku. Mwa anthu 100 odwala TB, 95 akukhala m’mayiko amene akutukuka kumene. Tsopano anthu 20 miliyoni akudwala TB yofalitsidwa, ndipo anthu ena okwana 30 miliyoni mwina adzafa nayo zaka khumi zikubwerazi, anthu okwanira chiŵerengero cha anthu onse a m’dziko la Bolivia, Cambodia, ndi Malaŵi.

N’zosadabwitsa kuti mu 1997 bungwe la WHO linali losangalala kuulutsa kuti lapanga njira yochizira TB m’miyezi isanu popanda kukam’goneka wodwalayo m’chipatala, kapena kugwiritsa ntchito zipangizo zachipatala zapamwamba. Buku lina lotchedwa The TB Treatment Observer, limene linafalitsidwa ndi bungwe la WHO, linanena kuti “kwa nthaŵi yoyamba, dziko latulukira zida ndiponso njira zinazake kuti lichiritse mliri wa TB osati m’mayiko olemera okha ayi, komanso ngakhale m’mayiko osauka kwambiri.” Njira imeneyi—imene ena aitcha kuti “imodzi mwa njira zofunika kwambiri zimene zatulukiridwa pa zaumoyo wa anthu kuchokera pa zaka khumi zapitazo mpaka lero”—imatchedwa DOTS.e

Ngakhale kuti mtengo wa chithandizo chimenechi ndi wochepa kwambiri kuyerekezera ndi wa chithandizo cha mankhwala a TB chimene chikugwiritsidwa ntchito kwambiri, zotsatirapo zake zili zolimbitsa mtima, makamaka kwa anthu amene akukhala m’mayiko amene akutukuka kumene. “Palibenso njira ina iliyonse yogonjetsera matenda a TB imene yakhala ikuchiritsa anthu kwambiri chonchi,” akutero Dr. Arata Kochi, woyang’anira ntchito yogonjetsa TB padziko lonse m’bungwe la WHO. “Ngakhale m’mayiko osaukitsitsa njira ya DOTS imachiritsa mpaka kufika 95 peresenti ya odwala.” Pakutha kwa chaka cha 1997, njira ya DOTS inali itayamba kugwiritsidwa ntchito m’mayiko 89. Lero chiŵerengero chimenecho chakwera n’kufika pa 96. Bungwe la WHO likuyembekezera kuti njira imeneyi ifikanso kwa anthu ena mamiliyoni ambiri amene ali osauka m’mayiko amene akutukuka kumene, kotero kuti athe kufupikitsa chotsekereza chachitatu pa liŵiro la moyo limeneli.

Mwa kusintha zizoloŵezi zake, kukonza malo ake okhala, ndi kukhala ndi chisamaliro chabwino cha zachipatala, munthu wathadi kuwonjezera utali umene anthu ambiri amatha kukhala ndi moyo ndiponso utali wa moyo umene munthu amayembekezereka kukhala. Funso lilipo ndi lakuti, Kodi zidzatheka kuti tsiku lina munthu adzathe kutalikitsa malekezero a moyo wa munthu—kuti mwina mpaka n’kukhala ndi moyo wopanda malire?

[Mawu a M’munsi]

a Ngakhale kuti mawu akuti “moyo umene munthu amayembekezereka kukhala” ndi akuti “utali umene anthu ambiri amatha kukhala ndi moyo” nthaŵi zambiri amatchulidwa ngati amodzi, mawu aŵiri ameneŵa ndi osiyana. Mawu akuti “moyo umene munthu amayembekezereka kukhala” amatanthauza kuchuluka kwa zaka zimene munthu angayembekezere kukhala ndi moyo, pamene mawu akuti “utali umene anthu ambiri amatha kukhala ndi moyo” amatanthauza kuchuluka kwa zaka zimene anthu ena ake paokhapaokha amakhaladi ndi moyo. Motero, chiŵerengero chongoyerekezera cha moyo umene munthu amayembekezereka kukhala chimapezedwa poona utali umene anthu ambiri amatha kukhala ndi moyo.

b Kuphatikizapo zinthu zimenezi zimene zingathe kusinthidwa, chibadwa chimene chili chosasintha mosakayikira chimakhudza thanzi lake ndiponso utali wa moyo wake. Zimenezi zikambidwa m’nkhani yotsatira.

c Ngati mukufuna kudziŵa zambiri zokhudza mmene mungakonzere mosavuta malo anu okhala, onani nkhani zakuti “Kukumaniza Chitokoso cha Udongo” ndi ina yakuti “Zimene Zimakupatsani Thanzi—Zimene Mungachite,” mu nkhani za Galamukani! za September 8, 1998 ndi April 8, 1995.

d Malo amene Mboni za Yehova zimachitirako misonkhano yawo ya mlungu uliwonse amatchedwa Nyumba ya Ufumu. Aliyense angathe kubwera ku misonkhano imeneyi, ndipo sikukhala nthaŵi ya zopereka.

e DOTS ndi chidule cha mawu akuti directly observed treatment, short-course. (Chithandizo Choyang’aniridwa Mwachindunji, Mankhwala Achidule) Kuti mudziŵe zambiri zokhudza njira ya DOTS. Onani nkhani yakuti “Njira Yatsopano Yolimbana ndi Matenda a TB, m’magazini ya Galamukani! ya June 8, 1999.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

UTALI NDI MTUNDU WA KULIMBITSA THUPI UKHALE WOTANI?

“Kukhala ndi cholinga cha kuchita maseŵera koma mosapambanitsa kwa mphindi 30 patsiku ndi bwino,” likutero bungwe loona za anthu okalamba lotchedwa National Institute on Aging (NIA). Koma simuyenera kuti muchite maseŵera olimbitsa thupi kwa mphindi 30 zimenezi nthaŵi imodzi ayi. Kuchita maseŵera olimbitsa thupi katatu kwa mphindi 10 nthaŵi iliyonse akuti ndi kopindulitsa mofanana ndi mmene kulili kuchita maseŵera a mtundu womwewo kwa mphindi 30. Kodi ndi mtundu wanji wa maseŵera olimbitsa thupi amene mungachite? Kabuku ka bungwe la NIA kotchedwa Don’t Take It Easy: Exercise! kakuvomereza kuti: “Ngati mutamachita ntchito ya nthaŵi yochepa, monga kukwera masitepe m’malo mwa chikepe, kapena kuyenda pansi m’malo mokwera galimoto, mungathe kukwanitsa mphindi 30 za ntchito yolimba. Ntchito monga kusesa zinyalala, kuchita maseŵera odzetsa thukuta ndi ana, kulima dimba, ngakhale ntchito zina za panyumba mungazichite kotero kuti pakutha kwa tsiku lililonse mungakwanitse mphindi zimenezi.” Inde, ndi chinthu chanzeru kuyamba mwafunsa kaye dokotala musanayambe makonzedwe akuti muzichita maseŵera olimbitsa thupi alionse.

[Chithunzi]

Ntchito yolimba yosapambanitsa ingathe kuthandiza anthu achikulire kuti akhale ndi nyonga komanso moyo wa mphamvu

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

KUFEŴETSA MAGANIZO ANU

Asayansi atafufuza mwa anthu achikulire zikwi zambiri anapeza zinthu zingapo zimene zimathandiza kufeŵetsa maganizo a munthu wachikulire. Zina ndi monga “kuŵerenga mofuna kumvetsa, kuyenda maulendo, zochitika zokhudza chikhalidwe, maphunziro, magulu ochita zinthu zinazake, ndi misonkhano yokhudza ntchito imene amagwira.” “Chitani chilichonse chimene mungathe.” “Pitirizani ntchito yanu. Osapuma. “Zimitsani TV.” “Phunzirani ntchito inayake.” Akuti zimenezi zimathandiza kuti munthu akhale osangalala komanso zimakonza molumikizira manyuroni a m’bongo.

[Chithunzi patsamba 7]

Kugwiritsa ntchito maganizo kumathandiza kuganiza bwino

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

MALANGIZO A ZATHANZI KWA OKALAMBA

Bungwe loona za anthu okalamba lotchedwa National Institute on Aging, limene lili gawo la U.S. Department of Health and Human Services, linanena kuti “mwayi wokhala ndi thanzi ndiponso kukhala ndi moyo wautali ungathe kuwonjezedwa” potsatira malangizo anzeru, monga ngati aŵa:

● Idyani zakudya za magulu atatu, ndiponso zipatso ndi masamba.

● Ngati mumamwa moŵa, muyenera kumwa mosapambanitsa.

● Osasuta fodya. Sikuti mwafika poti simungasiye ayi.

● Chitani maseŵera olimbitsa thupi pafupipafupi. Onanani ndi dokotala musanachite makonzedwe akuti muzichita maseŵera olimbitsa thupi.

● Osatayana nawo abale anu ndi anzanu.

● Gwiranibe ntchito, seŵerani, ndiponso kuthandiza nawo pa ntchito za m’mudzi kuti mukhalebe amphamvu.

● Pitirizanibe kuona kusangalatsa kwa moyo.

● Chitani zinthu zimene mumasangalala nazo.

● Pitani kukayezetsa thanzi lanu kaŵirikaŵiri.

[Bokosi patsamba 9]

MASELO A MUUBONGO AWONEDWA MWATSOPANO

“Poyamba tinkaganiza kuti munthu amataya maselo a muubongo paliponse muubongo wake,” akutero Dr. Marilyn Albert, polofesa wina wa maphunziro a nthenda za maganizo ndi za ubongo. “Koma si choncho ngakhale pang’ono—inde munthu akamakalamba amataya maselo a ubongo ngakhale ali bwinobwino, koma sikuti amakhala ambiri, ndipo amangokhala patalipatali chabe m’mbali zina chabe za ubongo.” Ndiponso, zimene zatulukiridwa posachedwapa zikuonetsa kuti ngakhale zimene anthu akhala akukhulupirira kwa nthaŵi yaitali zakuti anthu sangathe kumeranso maselo a ubongo atsopano, ndi kukulitsa chabe nkhani, “ngati kuti nthaŵi zonse zimachitika choncho,” akutero magazini a Scientific American a November 1998. Asayansi ya ubongo akunena kuti tsopano apeza umboni wakuti ngakhale anthu okalamba “amapanga manyuroni atsopano mazanamazana.”

[Bokosi patsamba 11]

WAMKULU NDIPONSO WANZERU?

“Kodi palibe nzeru pakati pa okalamba ndiponso luntha m’masiku ochuluka?” Baibulo limafunsa motero. (Yobu 12:12, NW) Kodi yankho lake ndi lotani? Anthu ofufuza anapenda anthu achikulire kuti aone zinthu ngati “nzeru, kuganiza bwino, kutulukira zinthu zosiyana ndi kuzipenda mosamala, ndi kupeza njira zabwino zothetsera vuto.” Malingana ndi zimene U.S News & World Report inanena kufufuzako kunasonyeza kuti “anthu achikulire apitirizabe kupambana achinyamata pa nzeru zilizonse. Iwo akhala akupereka malangizo oganiziridwa bwino, ndiponso anzeru.” Kufufuza kwina kukusonyezanso kuti “ngakhale kuti nthaŵi zambiri anthu achikulire amachedwa kusankha chochita, nthaŵi zambiri amasankha bwinopo poyerekeza ndi zimene achinyamata amasankha.” Motero monga mmene buku la m’Baibulo la Yobu likunenera, n’zoonadi kuti munthu wa zaka zambiri ndi munthu wanzeru.

[Chithunzi patsamba 5]

Moyo wa munthu uli ngati liŵiro lokhala ndi zotsekereza njira zambirimbiri

[Chithunzi patsamba 9]

“Dzichititseni kuti anthu azisangalala akakhala nanu,” akulangiza motero mayi wina wamasiye

[Chithunzi patsamba 10]

“Kuthandiza ena kudziŵa tanthauzo lenileni la moyo ndi ntchito yokhutiritsa.”—Evelyn

[Chithunzi patsamba 10]

“Ku Nyumba yathu ya Ufumu, ndimasangalala kwambiri poyankhula ndi ena, achikulire ndi achinyamata omwe.”—Louise

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena