Mungathandizidwe Kumvetsetsa Baibulo
M’Baibulo muli zinthu zofunika kwambiri kwa inu.
• Limafotokoza zimene Mlengi amanena za cholinga cha moyo.
• Limapereka malangizo abwino kwambiri a zimene mungachite kuti muthe kulimbana ndi mavuto pa moyo wanu panopa.
• Limafotokoza zimene tiyenera kuchita kuti tidzakhale ovomerezeka kwa Mulungu akamadzaweruza anthu onse.
Maphunziro a Baibulo opitirira 5,000,000 akuchitika padziko lonse.
Nthaŵi ndi malo ochitira zimakhala zimene inuyo mungakonde. Phunzirolo N’LAULERE.
Tumizani pempho lanu ku adiresi ya kufupi ndi kwanu pa maadiresi amene ali m’munsiŵa, kapena funsani Mboni ya Yehova iliyonse m’dera lanu.