Kuchotsa Osalapa
N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuteteza mpingo ku zinthu zoipa?
Kodi khalidwe loipa la m’bale kapena mlongo lingakhudze bwanji mpingo wonse?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yos 7:1, 4-14, 20-26—Tchimo limene Kaini ndi banja lake anachita linachititsa kuti mtundu wonse ukumane ndi mavuto
Yon 1:1-16—Mneneri Yona akanaphetsa anthu onse omwe anali naye muboti chifukwa cha kusamvera kwake
Kodi Mkhristu ayenera kupewa makhalidwe ati kuti asachotsedwe mumpingo?
N’chiyani chiyenera kuchitika ngati Mkhristu wobatizidwa akupitirizabe kuchita tchimo lalikulu?
Akamasamalira nkhani ya munthu yemwe wachita tchimo lalikulu, kodi akulu ayenera kukumbukira mfundo za mʼBaibulo ziti?
N’chifukwa chiyani kuchotsa kapena kudzudzula anthu ena mumpingo n’koyenera? Nanga zimenezi zingathandize bwanji mpingo?
Kodi Baibulo limanena kuti tizichita bwanji zinthu ndi anthu ochotsedwa?
Kodi munthu yemwe anachotsedwa akalapa, zingatheke kuti abwerere mumpingo?
Onaninso “Kulapa”
Kodi tonsefe tingathandize bwanji kuti mpingo upitirize kukhala woyera?
Onaninso De 13:6-11
N’chifukwa chiyani kungakhale kulakwitsa ngati Mkhristu atabisa tchimo lalikulu mwina chifukwa choopa kuchotsedwa?
Sl 32:1-5; Miy 28:13; Yak 5:14, 15
Onaninso “Tchimo—Kuulula Machimo”