Zitsanzo za Ulaliki
Uthenga wa Ufumu Na. 38
“Ndikugwira nawo ntchito imene ikuchitika padziko lonse, youza anthu uthenga wofunika kwambiri. Uthenga wake uli pakapepala aka.”
Dziwani izi: Muzilankhula mwachidule kwambiri n’cholinga choti mumalize gawo lonse. Komabe, nthawi zina mungapeze munthu wachidwi kwambiri amene angafune kuti mukambirane naye. Mukapeza munthu wotero, mungamupemphe kuti afotokoze maganizo ake pa funso limene lili patsamba loyamba, kenako mungawerenge naye yankho la m’Baibulo limene lasonyezedwa m’kati mwa kapepalako. Ngati nthawi ilipo mungawerenge nayenso gawo lina pakapepalako. Musanasiyane ndi munthuyo, musonyezeni funso limene lili patsamba lomaliza la kapepalako, pansi pa mutu wakuti “Ganizirani Mfundo Iyi.” Kenako mugwirizane zoti mudzabwerenso n’kudzapitiriza kukambirana naye.
Nsanja ya Olonda November 1
“Kodi inuyo mukuganiza kuti ndi bodza lalikulu liti limene anthu amanena lokhudza Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amafuna zoti anthu azimukonda komanso kumukhulupirira. [Werengani Yesaya 41:13.] Magaziniyi ikusonyeza mabodza atatu okhudza Mulungu amene anthu ena amanena, omwe amachititsa kuti anthu asamamukhulupirire.”
Galamukani! November
“Anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa chakuti makhalidwe abwino akulowa pansi. Kodi inuyo mukuganiza kuti ndi zoona kuti makhalidwe abwino akulowa pansi? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo linalosera kuti maganizo komanso makhalidwe a anthu adzasintha. [Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.] Magazini iyi ikusonyeza chifukwa chake tingadalire mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo.”