NKHANI YOPHUNZIRA 46
NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”
Tiziganizira za Yesu Amene Ndi Mkulu wa Ansembe Wathu Yemwe Amatimvera Chisoni
“Mkulu wa ansembe amene tili nayeyu, si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu.”—AHEB. 4:15.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tikambirana chifukwa chake Yesu ali Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri kuposa aliyense amene tingakhale naye komanso mmene amatithandizira mwachifundo m’njira zosiyanasiyana masiku ano.
1-2. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Aheberi 5:7-9)
ZAKA pafupifupi 2,000 zapitazo, Yehova Mulungu anatumiza Mwana wake wamtengo wapatali padziko lapansi. Chifukwa chiyani? Zina mwa zifukwa zake ndi kudzapulumutsa anthu ku temberero la uchimo ndi imfa komanso kudzakonza zinthu zimene Satana anawononga. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 3:8) Yehova ankadziwanso kuti zimene Yesu akanaphunzira atabwera padzikoli n’kudzakhala munthu, zikanamuthandiza kuti akhale Mkulu wa Ansembe wachifundo amene angatimvere chisoni. Yesu anayamba kutumikira monga Mkulu wa Ansembe atabatizidwa mu 29 C.E.a
2 Munkhaniyi tikambirana zimene Yesu anakumana nazo atabwera padzikoli komanso mmene zinamuthandizira kuti akhale Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri, amene amatha kutimvera chisoni. Tikamvetsa bwino zimene zinathandiza Yesu kuti ‘akhale wangwiro n’kuyenerera udindo wakewu, zitithandiza kuti tisamavutike kupemphera kwa Yehova ngakhale pamene tili ndi chisoni chifukwa cha machimo athu kapena zimene timalakwitsa.—Werengani Aheberi 5:7-9.
MWANA WOKONDEDWA WA MULUNGU ANABWERA PADZIKO LAPANSI
3-4. Kodi zinthu zinasintha bwanji pa moyo wa Yesu atabwera padziko lapansi?
3 Ambirife zinthu zinasinthapo pa moyo wathu. Mwachitsanzo, tinasamukapo kumene tinkakhala n’kusiyana ndi achibale komanso anzathu. Kusintha kumeneku kumakhala kovuta. Koma palibe munthu amene zinthu zambiri zinasintha pa moyo wake kuposa Yesu. Ali kumwamba, anali mngelo wofunika kwambiri kwa Yehova kuposa angelo onse. Yesu ankakondedwa kwambiri ndi Yehova ndipo nthawi zonse ankasangalala akamagwira ntchito ‘kudzanja lamanja’ la Yehova. (Sal. 16:11; Miy. 8:30) Koma lemba la Afilipi 2:7 limanena kuti mofunitsitsa “anasiya zonse zimene anali nazo” ndipo anasiya malo ake apamwamba kumwamba n’kubwera padzikoli kumadzakhala ndi anthu.
4 Taganiziraninso zimene zinachitika Yesu atabadwa komanso ali mwana. Yesu anabadwira m’banja losauka ndipo nsembe imene makolo ake anapereka iye atabadwa imasonyeza zimenezo. (Lev. 12:8; Luka 2:24) Herode yemwe anali mfumu yoipa atadziwa zoti Yesu wabadwa, anayesetsa kuti amuphe. Kuti apulumutse Yesu m’manja mwa Herode, banja lawo linathawira ku Iguputo kumene anakakhalako kwakanthawi. (Mat. 2:13, 15) Moyo wa Yesu unasintha kwambiri atabwera padzikoli.
5. Kodi Yesu anakumana ndi zotani padzikoli, nanga zinamuthandiza bwanji kuti akhale wokonzeka kukhala Mkulu wa Ansembe? (Onaninso chithunzi.)
5 Yesu ali padzikoli, ankaona anthu ambiri akuvutika. Yesu ali padzikoli ankaona anthu ambiri akumwalira kuphatikizapo Yosefe amene anali bambo ake omulera. Akuchita utumiki wake, Yesu anakumanapo ndi anthu akhate, a vuto losaona, ofa ziwalo komanso makolo amene ana awo anamwalira. Ndipo anthu onsewo ankawamvera chisoni. (Mat. 9:2, 6; 15:30; 20:34; Maliko 1:40, 41; Luka 7:13) N’zoona kuti Yesu ali kumwamba ankaona anthu akuvutika. Koma atabwera padzikoli, anamvetsa bwino mmene anthu amamvera akamavutika. (Yes. 53:4) Zimene anakumana nazo atabwera padzikoli zinamuthandiza kumvetsa mmene anthu amamvera, mmene zimakhalira akakhumudwa komanso ululu umene amamva chifukwa cha mavuto. Yesu ankakumana ndi mavuto amene anthufe timakumana nawo monga kutopa, kukhala ndi nkhawa komanso chisoni.
Yesu ankakhudzidwa kwambiri ndi mavuto amene anthu ankakumana nawo komanso mmene ankamvera (Onani ndime 5)
YESU AMAKONDA KWAMBIRI ANTHU
6. Kodi mawu amene mneneri Yesaya anagwiritsa ntchito akutiphunzitsa chiyani za chikondi ndi chifundo cha Yesu? (Yesaya 42:3)
6 Pa nthawi imene ankachita utumiki wake, Yesu ankachitira chifundo anthu onyozeka komanso amene ankachitiridwa nkhanza. Zimene anachitazi zinkakwaniritsa ulosi. M’Malemba a Chiheberi anthu amene ndi olimba mwauzimu, nthawi zina amawayerekezera ndi dimba lothiriridwa bwino kapena mitengo yaitali komanso yaikulu. (Sal. 92:12; Yes. 61:3; Yer. 31:12) Koma anthu osauka ndi oponderezedwa akuwayerekezera ndi bango lophwanyika komanso chingwe chanyale chimene chikufuka utsi, zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zosathandiza kwenikweni. (Werengani Yesaya 42:3; Mat. 12:20) Mouziridwa, mneneri Yesaya anagwiritsa ntchito mawu oyerekezera zinthuwa ponena za chikondi komanso chifundo chimene Yesu adzasonyeze anthu onyozeka omwe ena amawaona kuti ndi osafunika.
7-8. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi wa Yesaya?
7 Mateyu amene analemba buku la Uthenga Wabwino, anasonyeza kuti Yesu anakwaniritsa ulosi wa Yesaya pamene analemba kuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo chingwe cha nyale chimene chikufuka utsi sadzachizimitsa.” Zina mwa zozizwitsa zimene Yesu anachita zinathandiza anthu oponderezedwa amene ayenera kuti ankadziona ngati bango lophwanyika. Zinathandizanso anthu amene ankadziona kuti alibe chiyembekezo, omwe ankadzimva ngati chingwe cha nyale chimene chikufuka utsi chomwe chingazimitsidwe nthawi iliyonse. Mmodzi mwa anthuwa ndi munthu amene anali ndi khate thupi lonse. Iye ayenera kuti analibe chiyembekezo choti adzachira n’kumasangalala kukhala ndi banja lake komanso anzake. (Luka 5:12, 13) Panalinso munthu amene anali ndi vuto losamva komanso ankavutika kulankhula. Taganizirani mmene ankamvera akamaona anthu akuoneka kuti akulankhulana koma iye osamva kuti akulankhulana chiyani. (Maliko 7:32, 33) Koma panalinso anthu ena ambiri.
8 M’nthawi ya Yesu, Ayuda ambiri ankakhulupirira kuti anthu amene ankavutika chifukwa cha matenda kapena kulumala, ankakhala kuti akulangidwa chifukwa cha machimo amene iwowo kapena makolo awo anachita. (Yoh. 9:2) Chifukwa cha zinthu zolakwika zimene ankakhulupirirazi, anthu amene ankavutika ankadziona kuti ndi achabechabe. Pokwaniritsa ulosi wa Yesayawu, Yesu anachiritsa anthu amene ankadwala matenda osiyanasiyana ndipo anawathandiza kudziwa kuti Mulungu amawakonda. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?
9. Kodi lemba la Aheberi 4:15, 16, likusonyeza bwanji kuti Mkulu wa Ansembe wathu amachitira chifundo anthu opanda ungwirofe?
9 Werengani Aheberi 4:15, 16. Sitikayikira kuti nthawi zonse Yesu adzatisonyeza chifundo. Kodi munthu wachifundo amatani? Munthu wachifundo amakhudzidwa ndi mavuto komanso nkhawa za munthu wina. Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chifundo” amatanthauza kumva chisoni komanso ululu umene munthu wina akumva. (Onaninso pa Aheberi 10:34, pamene Paulo anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki omwewa.) Zozizwitsa zimene Yesu anachita, zimasonyeza mmene ankakhudzidwira ndi mavuto amene anthu ankakumana nawo. Iye sankangochiritsa anthu mwamwambo koma ankawakonda ndipo ankafunitsitsa kuwathandiza. Mwachitsanzo, pamene ankachiritsa munthu wakhate, Yesu akanatha kumuchiritsa ali chapatali. Koma anamugwira ndipo aka kayenera kuti kanali koyamba kuti munthu wakhateyo agwiridwe pambuyo pa zaka zambiri. Ndipo pamene Yesu ankachiritsa munthu amene anali ndi vuto losamva, anamuganizira pomuchotsa pagulu n’kukamuchiritsira kwayekha. Komanso pamene mayi wina amene poyamba ankachita zoipa koma n’kulapa anasambitsa mapazi a Yesu ndi misozi yake n’kuwapukuta ndi tsitsi lake, Mfarisi wina anamulankhula zinthu mopanda chilungamo. Koma Yesu anateteza mzimayiyo ndipo anadzudzula mwamphamvu Mfarisiyo. (Mat. 8:3; Maliko 7:33; Luka 7:44) Yesu sankapewa anthu amene ankadwala kapena amene anachita machimo akuluakulu. M’malomwake ankawalandira mwachifundo ndipo anawathandiza kukhala ndi chiyembekezo. Sitikukayikira kuti nafenso amatichitira chifundo.
MUZITSANZIRA MKULU WA ANSEMBE WATHU
10. Kodi ndi zinthu zauzimu ziti zimene tingagwiritse ntchito masiku ano pothandiza anthu a vuto losamva komanso losaona? (Onaninso zithunzi.)
10 Monga otsatira a Yesu okhulupirika, timayesetsa kusonyeza chikondi komanso chifundo kwa ena. (1 Pet. 2:21; 3:8) Ngakhale kuti sitingathe kuchiritsa anthu a vuto losamva komanso losaona, tikhoza kuwathandiza mwauzimu. Mwachitsanzo, mabuku othandiza pophunzira Baibulo akupezeka m’zinenero za manja zoposa 100. Ndipo pofuna kuthandiza anthu amene ali ndi vuto losaona, mabuku othandiza anthuwa akupezeka m’zinenero zoposa 60 ndipo mawu ofotokozera mavidiyo amajambulidwa m’zinenero zoposa 100. Zinthuzi zikuthandiza anthu a vuto losamva komanso losaona kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso Yesu.
Mabuku athu othandiza pophunzira Baibulo akupezeka m’zilankhulo zoposa 1,000
Kumanzere: Mabuku a zinenero zamanja zoposa 100
Kumanja: Mabuku a zilankhulo za anthu a vuto losaona zoposa 60
(Onani ndime 10)
11. Kodi gulu la Yehova limatsanzira bwanji chifundo cha Yesu pothandiza anthu amitundu yonse? (Machitidwe 2:5-7, 33) (Onaninso zithunzi.)
11 Gulu la Yehova limayesetsa kuthandiza anthu amitundu yonse. Kumbukirani kuti Yesu ataukitsidwa, anapereka mzimu woyera kwa onse amene anapezeka pa chikondwerero cha Pentekosite moti aliyense ankamva uthenga wabwino “mʼchilankhulo chake.” (Werengani Machitidwe 2:5-7, 33.) Potsanzira Yesu, gulu la Yehova limapereka mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zilankhulo zoposa 1,000 ndipo zina mwa zilankhulozi zimalankhulidwa ndi anthu ochepa. Mwachitsanzo, zilankhulo zina za Chiamerindiani zimalankhulidwa ndi anthu ochepa kwambiri omwe amakhala kumpoto ndi kum’mwera kwa America. Koma mabuku athu akupezeka m’zilankhulo za Chiamerindiani zoposa 160 n’cholinga choti anthu ambiri akhale ndi mwayi womva uthenga wathu. Mabuku athu amapezekanso m’zilankhulo za Chiromane zoposa 20. Anthu masauzande olankhula zilankhulo zimenezi ayamba kutumikira Yehova.
Kumanzere: Mabuku a zilankhulo za Chiamerindiani zoposa 160
Kumanja: Mabuku a zilankhulo za Chiromane zoposa 20
(Onani ndime 11)
12. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene gulu la Yehova limatipatsa?
12 Kuwonjezera pamenepa, gulu la Yehova limathandizanso anthu amene akuvutika chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe. Ndipotu pali anthu masauzande amene amadzipereka kuti athandize abale ndi alongo awo amene akufunika thandizo. Komanso gulu la Yehova limatipatsa malo abwino olambirira amene timasonkhana n’kumaphunzira za chikondi cha Mulungu.
MKULU WA ANSEMBE WATHU ANGAKUTHANDIZENI
13. Kodi ndi njira zina ziti zimene Yesu amatithandizira?
13 Monga m’busa wathu wabwino, Yesu amaonetsetsa kuti tili ndi zinthu zotithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Yoh. 10:14; Aef. 4:7) Nthawi zina mavuto amene timakumana nawo, amatipangitsa kuti tizidzimva ngati ndife chingwe cha nyale chimene chikufuka utsi kapena bango lophwanyika. Tikhoza kukhumudwa chifukwa cha matenda aakulu, zimene talakwitsa kapena ngati tasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzathu. Tikhozanso kuvutika kusiya kuganizira za ululu umene tikumva n’kumaganizira zinthu zabwino zam’tsogolo. Koma muzikumbukira kuti Yesu amaona zimene mukukumana nazo ndipo amamvetsa maganizo amumtima mwanu. Yesu ndi wachifundo ndipo adzatithandiza. Mwachitsanzo, akhoza kugwiritsa ntchito mzimu woyera kuti akupatseni mphamvu mukafooka. (Yoh. 16:7; Tito 3:6) Yesu angagwiritsenso ntchito amuna amene ndi “mphatso” komanso Akhristu anzathu kuti atilimbikitse ndi kutithandiza.—Aef. 4:8.
14. Kodi tingatani ngati takhumudwa?
14 Ngati tikudzimva ngati nyale imene ikuzima kapena bango lophwanyika, tiziganizira za Yesu yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wathu. Muzikumbukira kuti Yehova sikuti anangotumiza Yesu padzikoli kuti adzapereke moyo wake monga dipo basi, koma ankafunanso kumuthandiza kuti adzamvetse bwino mavuto amene anthufe timakumana nawo. Tikakhumudwa chifukwa cha machimo kapena zimene timalakwitsa, Yesu ndi wokonzeka komanso wofunitsitsa kutithandiza “pa nthawi yoyenera.”—Aheb. 4:15, 16.
15. Fotokozani chitsanzo chosonyeza mmene munthu amene wasochera m’gulu la Yehova angathandizidwire n’kubwereranso mumpingo.
15 Yesu amatsogoleranso anthu ake akamayesetsa kufunafuna komanso kuthandiza nkhosa za Yehova zosochera. (Mat. 18:12, 13) Taganizirani zimene zinachitikira Stefanob amene anachotsedwa mumpingo. Patadutsa zaka 12, iye anaganiza zopita kumisonkhano ndipo anati: “Zinali zovuta. Koma ndinkafuna kukhalanso m’banja la Yehova lachikondi. Akulu amene ndinakumana nawo anandithandiza kuti ndikhale womasuka. Nthawi zina maganizo odziona kuti ndine wachabechabe ankandibwerera ndipo ndinkangofuna kusiya. Koma abalewo anandikumbutsa kuti Yehova ndi Yesu ankafuna kuti ndisagwe ulesi. Nditabwezeretsedwa, mpingo wonse unatilandila limodzi ndi banja langa ndi manja awiri. Patapita nthawi, mkazi wanga analola kuti aziphunzira Baibulo ndipo panopa tikutumikira Yehova limodzi.” Mkulu wa Ansembe wathu yemwe ndi wachikondi amasangalala kwambiri akaona anthu omwe alapa akuthandizidwa kubwerera mumpingo.
16. N’chifukwa chiyani mumayamikira kukhala ndi Mkulu wa Ansembe amene amatimvera chisoni?
16 Yesu ali padzikoli anathandiza anthu ambiri pa nthawi yoyenera. Masiku ano sitikayikira kuti adzatithandiza nthawi iliyonse imene tikufunikira kuthandizidwa. Ndipo m’dziko latsopano limene latsala pang’ono, adzathandiza anthu omvera kuti asakhalenso pa ukapolo wa uchimo komanso kupanda ungwiro. Tikuyamikira Yehova amene chifukwa cha chikondi chake chachikulu komanso chifundo anasankha Mwana wake kuti akhale Mkulu wa Ansembe wathu amene amatimvera chisoni.
NYIMBO NA. 13 Titsanzire Yesu
a Kuti mudziwe zambiri za mmene udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe unalowedwera m’malo ndi udindo wa mkulu wa ansembe wa Chiyuda, onani nkhani yakuti, “Muziyamikira Mwayi Wanu Wolambira M’kachisi Wauzimu wa Yehova” mu Nsanja ya Olonda ya October 2023 tsamba 26, ndime 7-9.
b Dzina lasinthidwa.