Zimene Zingathandize Akazi Omwe Akuchitiridwa Nkhanza
“AMAYI ndi atsikana mamiliyoni padziko lonse amachitiridwa nkhanza. Kodi inunso munachitiridwapo nkhanza? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amaona kuti muyenera kutetezedwa komanso zimene adzachite pothetsa nkhanza zonse zimene anthu amachitira akazi.”
Amenewa ndi mawu oyambirira amene ali munkhani ya pawebusaiti ya jw.org ya mutu wakuti, “Kuteteza Akazi—Zimene Baibulo Limanena.” Linki imene ili kumapeto kwa nkhaniyo imakuthandizani kuti muthe kupanga dawunilodi nkhaniyi, kuipulinta n’kuipinda m’njira yoti ikhale pepala la masamba 4. Mlongo wina wa ku United States dzina lake Stacy ananena kuti: “Nditapulinta mapepalawa, ine ndi mlongo wina tinapita kumalo ena amene amasungira amayi amene amachitiridwa nkhanza, omwe ali m’gawo la mpingo wathu.”
Mayi wina amene amagwira ntchito pamalowa anapempha ngati pangapezeke mapepala ena amene angakagawire amayi amene amakhala kumalowa. Zotsatira zake mapepala enanso oposa 40 anatumizidwa kumalowa limodzi ndi makadi 30 othandiza anthu kudziwa za jw.org. Atapitanso ulendo wotsatira, woyang’anira malowa anapempha kuti a Mboniwo asonyeze anthu amene amakhala kumalowo mmene amaphunzirira Baibulo.”
Stacy ndi alongo ena awiri anakumananso ndi zofananazi pamene anapita kumalo ena amene amasungira amayi amene amachitidwa nkhanza kumene anagawira mapepala 5 ndipo anthuwo anapemphanso mapepala ena owonjezera. Mmodzi mwa ogwira ntchito kumaloko ananena kuti: “Kapepalaka kathandiza kwambiri azimayi kuno,” anapitiriza kuti: “Zimenezi ndi zimene timafunikira.” Pa ulendo wotsatira, anthu ambiri amene amakhala kumalowa anasonkhana kuti aone mmene phunziro la Baibulo limachitikira ndipo anthu awiri mwa anthu amenewa anasonyeza chidwi chofuna kudzapezeka nawo pamisonkhano ya kumapeto kwa mlungu ku Nyumba ya Ufumu.
Stacy ananena kuti: “Tachita chidwi ndi mmene anthu asangalalira kulandira nkhani imeneyi. Taona kuti tikapulinta komanso kupinda kapepalaka, ikumakhala njira yabwino kwambiri yolalikirira uthenga wabwino wa Ufumu kwa azimayi amenewa, omwe akuchitiridwa nkhanza. Zinatikhudza kwambiri kuona mmene anthuwo anasangalalira ndipo zinali zosangalatsa kuona mmene Yehova anadalitsira khama lathu kuti tifikire anthu amenewa ndi uthenga wabwino.”