Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 December tsamba 8-13
  • Buku la Yobu Lingatithandize Tikamapereka Malangizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Buku la Yobu Lingatithandize Tikamapereka Malangizo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MMENE ANZAKE ATATU A YOBU ANAMUPATSIRA MALANGIZO
  • MMENE ELIHU ANAPEREKERA MALANGIZO KWA YOBU
  • PITIRIZANI KUPHUNZIRA MFUNDO ZOTHANDIZA ZIMENE ZILI M’BUKU LA YOBU
  • Phunziro pa Kusamalira Mavuto
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mphotho ya Yobu—Magwero a Chiyembekezo
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 December tsamba 8-13

NKHANI YOPHUNZIRA 49

NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika

Buku la Yobu Lingatithandize Tikamapereka Malangizo

“Tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga.”—YOBU 33:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene buku la Yobu lingatithandizire kuti tizipereka malangizo abwino.

1-2. Kodi ndi vuto liti limene anzake atatu a Yobu komanso Elihu anakumana nalo?

NKHANI yokhudza Yobu inafalikira ngati moto wolusa kwa anthu akum’mawa. Munthu wotchuka komanso wolemera kwambiriyu anataya chilichonse. Anzake atatu omwe ndi Elifazi, Bilidadi ndi Zofari atamva zimene zinamuchitikira anapita ku Uzi kuti akamulimbikitse. Atafika anadabwa kuona zimene zinachitikira Yobu.

2 M’kanthawi kochepa, Yobu anataya zonse zimene anali nazo. Ziweto zonse zimene anali nazo monga nkhosa, ng’ombe, ngamila komanso abulu zinabedwa. Ana ake onse anafa ndipo atumiki ake ambiri anaphedwa. Nyumba imene ana a Yobu anafera inasanduka bwinja. Pambuyo pokumana ndi zinthu zoipa zonsezi, Yobu anayamba kudwala matenda aakulu. Thupi lake linali zilonda zokhazokha ndipo ankamva ululu woopsa. Anzake atatu aja ali chapatali anamuona atakhala yekhayekha pa phulusa ali wachisoni kwambiri. Kenako iwo anakhala ndi Yobu kwa masiku 7 koma sanamulankhule chilichonse ngakhale kuti anali pa ululu waukulu. (Yobu 2:​12, 13) Pa nthawi ina wachinyamata wina dzina lake Elihu anafika ndipo anakhala nawo pafupi. Pamapeto pake, Yobu anayamba kulankhula ndipo anatemberera tsiku limene anabadwa komanso ankalakalaka atangofa. (Yobu 3:​1-3, 11) N’zachidziwikire kuti Yobu ankafunika kuthandizidwa. Zimene anthuwo akanalankhula komanso mmene akanazilankhulira zikanasonyeza ngati analidi anzake enieni komanso ngati ankakhudzidwa ndi zimene zinamuchitikira.

3. Kodi tsopano tikambirana chiyani?

3 Yehova anauzira Mose kuti alembe zimene anzake atatu a Yobu komanso Elihu ananena ndiponso kuchita. Tingachite bwino kukumbukira kuti zina mwa zimene Elifazi analankhula, anachita kuuziridwa ndi mzimu woipa. Koma zimene Elihu analankhula anachita kuuziridwa ndi Yehova. (Yobu 4:​12-16; 33:​24, 25) N’chifukwa chake sitimadabwa kuti ngakhale kuti m’buku la Yobu mumapezeka malangizo abwino kwambiri, mumapezekanso malangizo ena oipa kwambiri. Ngakhale zili choncho, bukuli lingatithandize tikafuna kupereka malangizo. Choyamba, tikambirana zitsanzo zoipa za anzake atatu a Yobu. Kenako tikambirana chitsanzo chabwino cha Elihu. M’chitsanzo chilichonse tiona mmene buku la Yobu likanathandizira Aisiraeli komanso mmene lingatithandizire masiku ano.

MMENE ANZAKE ATATU A YOBU ANAMUPATSIRA MALANGIZO

4. N’chiyani chinapangitsa kuti anzake atatu a Yobu alephere kumulimbikitsa? (Onaninso chithunzi.)

4 Baibulo limanena kuti anzake atatu a Yobu atamva zinthu zoipa zimene zinamuchitikira, anapita kuti “akatonthoze Yobu ndi kumulimbikitsa.” (Yobu 2:11) Komabe analephera kumulimbikitsa. Chifukwa chiyani? Pali zifukwa zitatu. Choyamba analibe nthawi yomvetsera kuti adziwe mmene zinthu zinalili. Mwachitsanzo, iwo anali ndi maganizo olakwika akuti Yobu akulangidwa chifukwa cha machimo amene anachita.a (Yobu 4:7; 11:14) Chachiwiri, malangizo onse amene anzakewo anamupatsa anali osathandiza, opanda chifundo komanso opweteka kwambiri. Mwachitsanzo, zimene anzake atatuwo analankhula zimamveka ngati zabwino koma zinali zosathandiza ngakhale pang’ono. (Yobu 13:12) Mopanda chifundo, Bilidadi anauza Yobu kawiri konse, kuti akulankhula kwambiri. (Yobu 8:2; 18:2) Ndipo Zofari anayerekezera Yobu ndi “munthu wopanda nzeru.” (Yobu 11:12) Chachitatu, ngakhale kuti sankakweza mawu pamene ankalankhula ndi Yobu, zolankhula zawo komanso mmene ankalankhulira zinkasonyeza kuti ankamuimba mlandu, sankamulemekeza komanso sankamukonda. (Yobu 15:​7-11) M’malo momutonthoza komanso kumulimbikitsa, amunawa anapitiriza kuchita zinthu zosonyeza kuti Yobu ndi wolakwa.

Mmodzi mwa anzake a Yobu akumulankhula mawu opweteka pamene anzake ena awiri akungoyang’ana. Yobu yemwe ali ndi zilonda thupi lonse, akumvetsera zimene mnzakeyo akunena.

Mukamapereka malangizo musamapangitse munthu kuganiza kuti inuyo ndinu wabwino kwambiri kuposa iyeyo. Cholinga chanu chizikhala kumuthandiza (Onani ndime 4)


5. Kodi malangizo amene anzake a Yobu anamupatsa anamukhudza bwanji?

5 N’zosadabwitsa kuti malangizo amene anzake atatu a Yobu anapereka anali osathandiza. Mawu awo anamubaya Yobu. (Yobu 19:2) Mwina mukumvetsa chifukwa chake Yobu ankafotokoza mawu osonyeza kuti sanalakwe chilichonse. Zimenezi zinapangitsa kuti asokonezeke maganizo n’kulankhula mosaganiza bwino. (Yobu 6:​3, 26) Zimene anzake a Yobu ananena sizinali zogwirizana ndi maganizo a Yehova ndipo sanamuchitire zinthu mwachifundo. Zotsatira zake Satana anawagwiritsira ntchito kuti afooketse Yobu. (Yobu 2:​4, 6) Kodi nkhaniyi ikanathandiza bwanji anthu akale, nanga ingatithandize bwanji masiku ano?

6. Kodi akulu a ku Isiraeli akanaphunzira chiyani pa chitsanzo choipa cha anzake atatu a Yobu?

6 Mmene nkhaniyi ikanathandizira Aisiraeli. Atasankha mtundu wa Isiraeli, Yehova anasankhanso amuna oyenerera omwe anali akulu, kuti aziweruza mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. (Deut. 1:​15-18; 27:1) Amunawa ankayenera kumvetsera mosamala asanapereke malangizo kapena chiweruzo. (2 Mbiri 19:6) Ankafunikanso kufunsa mafunso m’malo mongoganiza kuti akudziwa nkhani yonse. (Deut. 19:18) Akuluwo ankafunika kupewa kulankhula mopanda chifundo kwa anthu amene ankabwera kuti awathandize. Chifukwa ngati sakanalankhula mokoma mtima zikanapangitsa kuti anthu alephere kulankhula momasuka zimene zili mumtima mwawo. (Eks. 22:​22-24) Zimenezi ndi zomwe akulu a ku Isiraeli akanaphunzira akanakhala kuti anawerenga nkhani ya m’buku la Yobu.

7. Kuwonjezera pa akulu a ku Isiraeli, ndi anthu enanso ati amene akanapereka malangizo, nanga nkhani ya Yobu ikanawathandiza bwanji? (Miyambo 27:9)

7 Si akulu okha amene ankafunika kupereka malangizo ku Isiraeli. Munthu aliyense kaya wamng’ono kapena wamkulu komanso mwamuna kapena mkazi akanatha kupereka malangizo kwa mnzake amene akufunika kusintha khalidwe lake kapena kuwonjezera zochita pa kulambira kwake. (Sal. 141:5) Kupereka malangizo mosapita m’mbali kumasonyeza kuti ndife anzawo abwino. (Werengani Miyambo 27:9.) Zitsanzo zoipa za anzake atatu a Yobu zikanathandiza Aisiraeli kudziwa zosayenera kulankhula komanso kuchita popereka malangizo.

8. Kodi timafunika kupewa zinthu ziti tikamapereka malangizo? (Onaninso zithunzi.)

8 Mmene nkhaniyi ingatithandizire. Monga Akhristu timafuna kuthandiza abale ndi alongo athu akamakumana ndi mavuto. Kuti zitheke, tingafunike kupewa zimene anzake atatu a Yobu anachita. Choyamba, tisamafulumire kupereka malangizo, m’malomwake tizifufuza kaye mosamala nkhani yonse. Chachiwiri, malangizo athu asamakhale ogwirizana ndi mmene ifeyo tikuonera zinthu ngati mmene Elifazi ankachitira nthawi zambiri, m’malomwake azikhala ochokera m’Mawu a Mulungu. (Yobu 4:8; 5:​3, 27) Chachitatu, tizipewa kulankhula mopanda chifundo komanso mokhadzula. Kumbukirani kuti Elifazi komanso anzake aja ananena zinthu zina zomwe zinali zolondola. Zina zimene ananena zinagwiritsidwa ntchito ndi munthu wina amene anauziridwa kulemba Baibulo. (Yerekezerani Yobu 5:13 ndi 1 Akorinto 3:19.) Komabe zinthu zambiri zimene ankanena zokhudza Yehova sizinali zolondola ndipo zinkavulaza Yobu, moti Yehova ananena kuti zinali zabodza. (Yobu 42:​7, 8) Malangizo abwino samachititsa anthu ena kuona kuti Yehova ndi wokhwimitsa zinthu kapena kupangitsa atumiki ake kumva kuti sakondedwa. Tiyeni tsopano tikambirane zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Elihu.

Zithunzi: M’bale akupereka malangizo mwachikondi kwa m’bale amene wakhumudwa. 1. M’bale akumvetsera moleza mtima pamene m’bale yemwe wakhumudwa akufotokoza zinthu, onse akhala patebulo panja kwinaku akumwa zoziziritsa kukhosi. 2. M’bale amene akumvetsera watsegula Baibulo. 3. M’bale akupereka malangizo mwachikondi kuchokera m’Baibulo, pamene m’bale wina akumvetsera modekha.

Mukamapereka malangizo, (1) muzifufuza kuti mudziwe bwino nkhani yonse, (2) muzigwiritsira ntchito Mawu a Mulungu ndipo (3) muzilankhula mwachikondi (Onani ndime 8)


MMENE ELIHU ANAPEREKERA MALANGIZO KWA YOBU

9. Fotokozani chifukwa chake Yobu ankafunika kuthandizidwa anzake atasiya kulankhula komanso mmene Yehova anamuthandizira.

9 Yobu ndi anzake atatu aja anakangana kwa nthawi yaitali. Iwo analankhula zinthu zambiri moti zinakwana machaputala 28 a m’Baibulo. Zambiri zomwe analankhula zimasonyeza kuti anali atakwiya komanso atakhumudwa. N’zosadabwitsa kuti Yobu anapitirizabe kumva ululu. Iye ankafunikabe kutonthozedwa komanso kuthandizidwa. Ndiye kodi Yehova anathandiza bwanji Yobu? Anagwiritsa ntchito Elihu kuti amupatse malangizo. N’chifukwa chiyani Elihu anadikira asanayambe kulankhula? Iye ananena kuti: “Ine ndine wamngʼono ndipo amuna inu ndinu achikulire. Nʼchifukwa chake mwaulemu ndinakhala chete.” (Yobu 32:​6, 7) Elihu ankadziwa mfundo imene ambiri amaidziwa masiku ano yakuti, achikulire amakhala ndi nzeru chifukwa akhala ndi moyo nthawi yaitali komanso akumana ndi zinthu zambiri pa moyo wawo kuposa achinyamata. Koma atamvetsera moleza mtima zimene Yobu ndi anzake aja analankhula, iye anaona kuti akufunika kulankhulapo. Iye anati: “Si zaka zokha zimene zimapangitsa kuti munthu akhale wanzeru, ndipo si achikulire okha amene amadziwa zinthu zoyenera.” (Yobu 32:9) Ndiyeno kodi kenako Elihu ananena chiyani, nanga anazinena bwanji?

10. Kodi Elihu anachita chiyani asanapereke malangizo kwa Yobu? (Yobu 33:​6, 7)

10 Elihu asanapereke malangizo kwa Yobu anaonetsetsa kaye kuti zinthu zili bwino. Kodi anachita bwanji zimenezi? Choyamba, anaonetsetsa kuti mtima wake uli m’malo. Tikudziwa zimenezi chifukwa Baibulo limanena kuti poyamba Elihu anakwiya. (Yobu 32:​2-5) Ngakhale kuti anakhumudwa, sanamulankhulepo Yobu mopanda chifundo koma ankamulimbikitsa. Mwachitsanzo, iye anamuuza Yobu kuti: “Inetu nʼchimodzimodzi ndi inu pamaso pa Mulungu woona.” (Werengani Yobu 33:​6, 7.) Kenako Elihu anamuuza Yobu kuti ankamumvetsera mosamala ndipotu asanamupatse malangizo, anabwereza mfundo zikuluzikulu zimene Yobu analankhula. (Yobu 32:11; 33:​8-11) Elihu anachitanso chimodzimodzi pa nthawi zina pamene ankamupatsa malangizo Yobu.—Yobu 34:​5, 6, 9; 35:​1-4.

11. Kodi Elihu anamupatsa bwanji Yobu malangizo? (Yobu 33:1)

11 Popereka malangizo kwa Yobu, Elihu ankamulemekeza munthu wokhulupirikayu. Mwachitsanzo, iye ankatchula dzina la Yobu koma zikuoneka kuti amuna atatu aja sanachite zimenezi. (Werengani Yobu 33:1.) Mwina pokumbukira kuti nayenso ankafuna kulankhulapo pamene Yobu ndi anzake aja ankakangana, Elihu anamupatsa mwayi Yobu kuti azilankhulapo pamene ankamupatsa malangizo. (Yobu 32:4; 33:32) Anamuchenjezanso Yobu kuopsa kwa zinthu zina zimene analankhula komanso kuchita ndipo mokoma mtima anamukumbutsa za makhalidwe a Yehova monga nzeru, mphamvu, chilungamo ndi chikondi chokhulupirika. (Yobu 36:​18, 21-26; 37:​23, 24) Mosakayikira malangizo abwinowa, anamuthandiza Yobu kuti akonzekere kulandira malangizo owonjezereka ochokera kwa Mlengi. (Yobu 38:​1-3) Kodi chitsanzo cha Elihu chikanathandiza bwanji anthu akale, nanga chingatithandize bwanji masiku ano?

12. Kodi Yehova ankagwiritsira ntchito bwanji aneneri kuthandiza anthu ake, nanga chitsanzo chabwino cha Elihu chikanathandiza bwanji Aisiraeli?

12 Kodi nkhaniyi ikanawathandiza bwanji Aisiraeli? Yehova nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito aneneri kuti aziphunzitsa komanso kupereka malangizo kwa Aisiraeli. Mwachitsanzo m’nthawi ya Oweruza, Yehova anagwiritsa ntchito mneneri wamkazi dzina lake Debora kuti apereke malangizo kwa anthu ake. Anagwiritsanso ntchito Samueli kuti azipereka malangizo kwa anthu ake kuyambira ali wamng’ono. (Ower. 4:​4-7; 5:7; 1 Sam. 3:​19, 20) M’nthawi ya mafumu, Yehova anapitiriza kugwiritsa ntchito aneneri kuti azithandiza anthu ake mwauzimu komanso kuti azipereka malangizo kwa anthu amene asiya kulambira koyera. (2 Sam. 12:​1-4; Mac. 3:24) Chitsanzo chabwino cha Elihu chimene chili m’buku la Yobu chikanathandiza amuna ndi akazi okhulupirika kudziwa zoyenera kunena akamapereka malangizo komanso mmene angachitire zimenezi mwachikondi.

13. Kodi Akhristu masiku ano angalimbikitse bwanji Akhristu anzawo?

13 Mmene nkhaniyi ingatithandizire. Monga Akhristu, ifenso timathandiza anthu ena kudziwa zimene Mulungu amafuna tikamawauza zimene zili m’Baibulo. Njira ina imene timachitira zimenezi ndi kugwiritsa ntchito mawu abwino potonthoza komanso kulimbikitsa Akhristu anzathu. (1 Akor. 14:3) Makamaka akulu akuyenera kukhala osamala kuti ‘azilankhula molimbikitsa’ kwa abale ndi alongo, ngakhalenso kwa amene asokonezeka maganizo ndipo ‘akulankhula mosaganiza bwino.’—1 Ates. 5:14; Yobu 6:3.

14-15. Kodi akulu angatsanzire bwanji chitsanzo cha Elihu akafuna kupereka malangizo?

14 Taganizirani chitsanzo ichi: Mkulu wadziwa kuti mlongo wina mumpingo mwawo akuvutika ndi nkhawa. Mkuluyo limodzi ndi m’bale wina apita kwa mlongoyo kukamulimbikitsa. Pocheza naye, iye akufotokoza nkhawa imene ali nayo kuti, ngakhale kuti nthawi zonse amapita kumisonkhano komanso mu utumiki, sasangalala kwenikweni. Kodi mkuluyo angatani?

15 Choyamba angayesetse kuti amvetse zifukwa zimene zikuchititsa mlongoyo kumva choncho. Angachite zimenezi pomumvetsera moleza mtima. Kodi mwina akukayikira zoti Yehova amamukonda? Kapena akulimbana ndi “nkhawa za moyo”? (Luka 21:34) Chachiwiri, mkuluyo angafunike kuyamikira mlongoyu chifukwa cha zabwino zimene amachita. Mwachitsanzo, angamuyamikire chifukwa chopitiriza kuchita khama mu utumiki komanso kusonkhana ngakhale kuti si zophweka kwa iyeyo. Ndipo chachitatu, mkuluyo akamvetsa mmene zinthu zilili komanso zifukwa zimene zikupangitsa mlongoyo kukhumudwa, angagwiritse ntchito Baibulo kuti amutsimikizire kuti Yehova amamukonda.—Agal. 2:20.

PITIRIZANI KUPHUNZIRA MFUNDO ZOTHANDIZA ZIMENE ZILI M’BUKU LA YOBU

16. Kodi tingatani kuti buku la Yobu lipitirize kutithandiza?

16 Pali zambiri zimene tingaphunzire kuchokera m’buku la Yobu. Munkhani yapita ija tinaphunzira chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika komanso zimene tingachite kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika tikamakumana ndi mavuto. Ndipo munkhaniyi taona kuti tonse tingakwanitse kupereka malangizo abwino ngati tingapewe kutsanzira chitsanzo choipa cha anzake atatu a Yobu, n’kumatsanzira chitsanzo chabwino cha Elihu. Ngati m’tsogolomu mungadzafunike kupereka malangizo kwa ena, mudzaganizire mfundo zimene mwaphunzira m’buku la Yobu musanapereke malangizowo. Ngati patenga nthawi musanawerenge buku losangalatsali, mungachite bwino kukonza zoti muliwerenge posachedwapa. Mudzaona kuti ndi lothandizanso masiku ano ngati mmene zinalili pa nthawi imene linkalembedwa.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera kwa anzake atatu a Yobu, pa zimene muyenera kupewa mukamapereka malangizo?

  • Kodi Elihu anasonyeza bwanji kuti ndi wanzeru pamene ankamupatsa Yobu malangizo?

  • Kodi tingatani kuti buku la Yobu lipitirizebe kumatithandiza?

NYIMBO NA. 125 “Osangalala Ndi Anthu Achifundo”

a Zikuoneka kuti mzimu woipa ndi umene unachititsa Elifazi kunena kuti Yehova saona munthu aliyense kuti ndi wolungama moti palibe amene angasangalatse Mulungu. Elifazi ankakhulupirira mfundo yabodzayi ndipo nthawi zonse akamalankhula ndi Yobu ankabwereza mfundo yolakwikayi.—Yobu 4:17; 15:​15, 16; 22:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena