Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 December tsamba 20-25
  • Zimene Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Lidzakhale Lolemekeza Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Lidzakhale Lolemekeza Yehova
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KULEMEKEZA YEHOVA PA TSIKU LA UKWATI?
  • ZIMENE MUNGACHITE KUTI MULEMEKEZE YEHOVA
  • ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUPEWE KOMANSO MUTHANE NDI MAVUTO
  • Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Maukwati Osangalatsa Amene Amalemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Maukwati Olemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 December tsamba 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 51

NYIMBO NA. 132 Tsopano Ndife Thupi Limodzi

Zimene Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Lidzakhale Lolemekeza Yehova

“Zinthu zonse zizichitika moyenera ndiponso mwadongosolo.”—1 AKOR. 14:40.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene Akhristu amene akufuna kulowa m’banja angachite kuti adzalemekeze Yehova pa tsiku laukwati wawo.

1-2. Kodi Yehova amafuna kuti pa tsiku laukwati pazichitika zotani?

KODI muli pachibwenzi ndipo mukukonzekera kulowa m’banja? Ngati ndi choncho, zabwino zonse. N’zoonekeratu kuti mwatanganidwa ndi kukonzekera ukwati wanu. Yehova akuchita chidwi ndi zimene mukuchita. Iye akufuna kuti tsiku la ukwatia wanu lidzakhale losangalatsa komanso mudzakhale ndi banja labwino.—Miy. 5:18; Nyimbo 3:11.

2 N’zofunika kwambiri kuti tsiku la ukwati wanu lidzalemekeze Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Nanga mungatani kuti zimenezi zidzatheke? Ngakhale kuti cholinga chachikulu cha nkhaniyi ndi kuthandiza anthu amene akukonzekera ukwati, mfundo zimene tikambirane zithandiza tonse kuti tizilemekeza Yehova tikapita ku ukwati kapena tikapemphedwa kuti tithandize munthu amene akukonzekera ukwati.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KULEMEKEZA YEHOVA PA TSIKU LA UKWATI?

3. Kodi Akhristu amene akukonzekera ukwati ayenera kuganizira zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Akhristu amene akukonzekera ukwati, ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo. Tikutero chifukwa Yehova ndi amene anayambitsa ukwati. Iye anamangitsa ukwati woyambirira wa Adamu ndi Hava. (Gen. 1:28; 2:24) Choncho amene akukonzekera ukwati ayenera kuchita zinthu zoti tsiku la ukwati wawo lidzalemekeze Yehova.

4. Kodi ndi zifukwa zina ziti zimene zingapangitse anthu amene akukonzekera ukwati kudzalemekeza Yehova pa tsiku la ukwati wawo?

4 Pali zifukwa zomveka zokupangitsani kuganizira mmene Yehova akumvera pa zimene mukufuna kudzachita pa ukwati wanu. Iye ndi Atate wanu wakumwamba ndipo mukufuna kuti apitirize kukhala Mnzanu wapamtima. (Aheb. 12:9) Simungafune kuti pa tsiku la ukwati wanu kapena pa tsiku lililonse pachitike chinthu chimene chingakhumudwitse Yehova, yemwe ndi Mnzanu. (Sal. 25:14) Mukaganizira zimene iye amakuchitirani, kodi simukuona kuti ndi woyenera kudzalemekezedwa pa tsiku la ukwati wanu?—Sal. 116:12.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MULEMEKEZE YEHOVA

5. Kodi Baibulo lingathandize bwanji amene akukonzekera ukwati kuti asankhe zinthu mwanzeru?

5 M’Baibulo mulibe m’ndandanda wa malamulo amene Akhristu ayenera kutsatira akamachita ukwati. Aliyense angasankhe mogwirizana ndi chikhalidwe chake, zimene amakonda komanso mmene zinthu zilili. Akhristu oona ayeneranso kutsatira malamulo aboma okhudza ukwati. (Mat. 22:21) Komabe kaya asankha zotani, ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti asangalatse komanso kulemekeza Yehova. Ndiye kodi ndi mfundo ziti zimene tiyenera kuziganizira?

6. N’chifukwa chiyani anthu amene akufuna kukwatirana ayenera kutsatira malamulo a boma okhudza ukwati?

6 Muzitsatira malamulo a boma okhudza ukwati. (Aroma 13:​1, 2) M’mayiko ena anthu amene akufuna kukwatirana amafunika kutsatira malamulo amene boma linakhazikitsa asanakwatirane. Iwo ayenera kufufuza malamulo amene amafunika kutsatira kwawoko. Ngati muli ndi mafunso pa nkhaniyi, mungafunse akulu.b

7. Kodi ukwati uyenera kuchitika bwanji?

7 Muzionetsetsa kuti ukwati wanu ukuchitika molemekezeka. (1 Akor. 10:​31, 32) Mudzaonetsetse kuti anthu akusonyeza makhalidwe abwino osati mzimu wadziko. (Agal. 5:​19-26) Malinga ndi mfundo ya m’Malemba yokhudza umutu, mwamuna ali ndi udindo woonetsetsa kuti ukwati wawo udzakhale wosangalatsa komanso wolemekezeka. Nkhani ya ukwati ikakambidwa mwachikondi komanso mwaulemu imathandiza anthu onse kudziwa kuti ukwati ndi nkhani yaikulu komanso ndi mphatso yochokera kwa Yehova. Choncho, Akhristu ambiri amasankha kuti nkhani ya ukwati wawo idzakambidwe ku Nyumba ya Ufumu. Ngati mukufuna zimenezi, mungalembe kalata mwachangu kwa akulu yopempha kuti mudzagwiritse ntchito Nyumba ya Ufumu.

8. Kodi mungatani kuti phwando la ukwati wanu likhale lolemekeza Yehova? (Aroma 13:13)

8 Werengani Aroma 13:13. Ngati mukufuna kudzakhala ndi phwando la ukwati, mungatani kuti anthu asadzasonyeze mzimu wadziko? Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “maphwando oipa” akunena za maphwando amene anthu amamwa mowa mopitirira malire komanso kumvetsera nyimbo mpaka pakati pa usiku. Ngati mwasankha kuti padzakhale mowa, mudzaonetsetse kuti anthu asadzamwe mopitirira malire.c Ngati padzakhale nyimbo, voliyumu isadzakhale yokwera kwambiri kuti anthu azidzatha kumvana akamacheza. Posankha nyimbo mungaganizirenso mtundu wa nyimbozo komanso uthenga wake kuti zisadzakhumudwitse ena.

9. Kodi amene akukonzekera kukwatirana ayenera kuganizira mfundo ziti pa nkhani ya amene adzalankhulepo komanso zosangalatsa zina?

9 Kodi mwasankha zoti anzanu kapena achibale adzalankhulepo, padzakhale mavidiyo, magemu kapena zinthu zina zosangalatsa? Izi zimapangitsa kuti tsikulo likhale losaiwalika. Komabe mudzaonetsetse kuti zinthu zimenezi zidzakhale zolimbikitsa. (Afil. 4:8) Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zilemekeza anthu ena? ‘Kodi zilemekeza dongosolo la ukwati?’ Ndipo funso lofunika kwambiri ndi lakuti: ‘Kodi zilemekeza Yehova?’ Ngakhale kuti nthabwala zina n’zabwinobwino, mudzaonetsetse kuti anthu sakulankhula chilichonse chimene chingapangitse ena kuganizira zokhudza kugonana. (Aef. 5:3) Mudzaonetsetse kuti achibale komanso anzanu amene munawasankha kuti adzalankhule adzalemekeze zosankha zanu.

10. N’chifukwa chiyani amene akufuna kukwatirana afunika kudzapewa kuchita zinthu modzionetsera pa tsiku la ukwati wawo? (1 Yoh. 2: 15-17)

10 Muzipewa kuchita zinthu modzionetsera. (Werengani 1 Yohane 2:​15-17.) Yehova amasangalala tikamachita zinthu zomulemekeza m’malo mofuna kuti anthu azingoganizira za ifeyo. Choncho Akhristu odzichepetsa amapewa kuwononga ndalama zambiri pongofuna “kudzionetsera.” Ngati mutakonza ukwati wosalira zambiri, mwina zomwe zingakuchitikireni zingafanane ndi zimene zinachitikira M’bale Mike wa ku Norway. Iye anati: “Tinalibe ngongole ndipo tinakwanitsa kupitiriza upainiya. Ukwati wathu sunali wapamwamba koma unali wosangalatsa komanso wosaiwalika.” Mlongo Tabitha wa ku India anati: “Tinakonza zoti ukwati wathu usadzakhale wapamwamba ndipo zinatithandiza kuti tisakhale ndi nkhawa. Tinalibe zambiri zoti tikonzekere choncho sitinkasemphana maganizo kwambiri.”

Zithunzi: Abale ndi alongo padziko lonse akusangalala pa ukwati. 1. Mkwati ndi mkwatibwi akhala pansi m’Nyumba ya Ufumu ndipo patsogolo pawo pali m’bale amene akukamba nkhani ya ukwati wawo. 2. Banja likufunira zabwino banja latsopano lomwe likuchitira panja mwambo wawo wa ukwati. 3. Mkwati ndi mkwatibwi ali pamzere ndipo akulandira chakudya pa phwando la ukwati wawo. 4. Mkwati ndi mkwatibwi aimirira ndipo patsogolo pawo pali m’bale amene akukamba nkhani ya ukwati wawo panja.

Posatengera kumene tikukhala, ukwati wa Akhristu ukhoza kukhala wosalira zambiri, wosangalatsa komanso wosaiwalika (Onani ndime 10-11)


11. Kodi mkwati ndi mkwatibwi angasonyeze bwanji kuti ndi osadzionetsera pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa? (Onaninso zithunzi.)

11 Kodi mwasankha kale zimene mudzavale? Sitikukayikira kuti pa tsikuli mukufuna mudzaoneke bwino kwambiri. Ngakhale anthu otchulidwa m’Baibulo ankavala bwino pa tsiku la ukwati wawo. (Yes. 61:10) N’zoona kuti zimene mungadzavale pa tsikuli zingadzakhale zapadera, komabe mukufunika kudzavala mwaulemu. (1 Tim. 2:9) Musadzalole kuti zimene mudzavale komanso mmene mudzadzikongoletsere chidzakhale chinthu chofunika kwambiri pa tsikuli.—1 Pet. 3:​3, 4.

12. N’chifukwa chiyani amene akufuna kukwatirana akuyenera kupewa miyambo ya ukwati yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo yomwe ndi yotchuka m’dera lawo?

12 Muzipewa miyambo yosemphana ndi mfundo za m’Malemba. (Chiv. 18:4) M’dzikoli anthu akamachita ukwati, amachitanso miyambo yokhudzana ndi chipembedzo chabodza komanso kukhulupirira mizimu. Yehova amatichenjeza momveka bwino kuti tisamachite nawo zinthu zodetsa zimenezi. (2 Akor. 6: 14-17) Ngati kwanuko kumachitika miyambo yaukwati imene mukuikayikira, mungafufuze kuti mudziwe mmene inayambira komanso mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru.

13. Kodi anthu amene akufuna kukwatirana angatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yolandira mphatso?

13 Kodi kumene mumakhala anthu amakonda kupereka mphatso pa ukwati? Mphatso zimene angapereke zimadalira m’thumba mwawo. N’zoona kuti Akhristu amalimbikitsidwa kukhala opatsa ndipo zimenezi zimawathandiza kuti azisangalala. (Miy. 11:25; Mac. 20:35) Komabe sitifunika kukakamiza anthu kupereka mphatso kapena kuona kuti mphatso yawoyo sikuyamikiridwa chifukwa si yapamwamba. Timatsanzira Yehova poyamikira mphatso iliyonse ndiponso posakakamiza ena kuti atipatse zomwe sangakwanitse.—2 Akor. 9:7.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUPEWE KOMANSO MUTHANE NDI MAVUTO

14. Kodi anthu ena amene akufuna kukwatirana amakumana ndi mavuto ati?

14 Mungakumane ndi mavuto pamene mukukonzekera kuti mudzakhale ndi ukwati wolemekezeka pamaso pa Yehova. Mwachitsanzo, sizophweka kuti mukonzekere ukwati wosalira zambiri. Charlie wa ku Solomon Islands anati: “Zinali zovuta kusankha anthu oti tiwaitane ku ukwati wathu. Tili ndi anzathu ambiri ndipo pachikhalidwe chathu aliyense amayembekezera kuitanidwa.” Tabitha, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Kumene ndimakhala anthu amakonda kuitana anthu ambiri ku ukwati. Panatenga nthawi kuti makolo athu afike povomereza zomwe tinasankha zoti tiitane anthu pafupifupi 100 basi.” Sarah wa ku India anati: “Anthu ambiri amakonda kuchita zinthu pofuna kudzionetsera kuti ali ndi ndalama. Makhazeni anga anapanga ukwati wapamwamba ndiye inenso ndinkafuna kuti ukwati wanga udzakhale wapamwamba kuposa wawo.” N’chiyani chingakuthandizeni kuti muthane ndi mavuto amenewa komanso ena?

15. N’chifukwa chiyani pemphero ndi lofunika kwambiri tikamakonzekera ukwati?

15 Mukamakonzekera ukwati muzipemphera. Tingamuuze Yehova zosankha zimene tikufuna kupanga komanso vuto lililonse limene takumana nalo tikamakonzekera ukwati. (Afil. 4:​6, 7) Tingamupemphenso kuti atithandize kusankha zinthu mwanzeru, kukhala odekha pamene tili ndi nkhawa komanso kuti tikhale olimba mtima ngati zimene tikufuna kusankha si zomwe anthu ena akufuna. (1 Pet. 5:7) Mudzayamba kudalira kwambiri Yehova mukaona kuti akukuthandizani. Tabitha yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ine ndi chibwenzi changa tinkaopa kuti tizisemphana maganizo komanso kusemphana maganizo ndi achibale athu. Choncho tikamakambirana za ukwati wathu tinkayamba ndi pemphero. Yehova ankatithandiza ndipo tinkakambirana mwamtendere.”

16-17. Kodi kulankhulana momasuka kungakuthandizeni bwanji pamene mukukonzekera ukwati?

16 Muzilankhulana momasuka komanso mwaulemu. (Miy. 15:22) Nonse awiri mukufunika kusankha zinthu zambiri zokhudza ukwati wanu. Zimenezi zikuphatikizapo deti la ukwati, ndalama zimene zidzafunike, anthu amene mudzawaitane komanso zinthu zina zambiri. Musanasankhe zochita, kambirananinso zimene mukufuna, mfundo za m’Baibulo zokhudza nkhaniyo komanso malangizo ochokera kwa Akhristu olimba mwauzimu. Mukamakambirana zimene mukufuna, muzifotokoza mwaulemu, muzikhala ololera komanso okonzeka kusintha. Ngati achibale kapena makolo akupemphani kuti mudzachite zinazake, mungayesetse kuchita zimene apemphazo. Tsiku limeneli ndi lapaderanso kwa iwowo. Koma ngati simungakwanitse zimene apemphazo, mungawafotokozere mwaulemu zifukwa zake. (Akol. 4:6) Muziwafotokozera momveka bwino kuti cholinga chanu chachikulu n’kudzakhala ndi ukwati wolemekeza Yehova.

17 Kufotokoza zimene mwasankha kwa makolo makamaka ngati si a Mboni, kungakhale kovuta kwambiri, komabe n’zotheka. M’bale Santhosh wa ku India, anati: “Achibale ankafuna kuti pa ukwati wathu tidzachite miyambo ina ya Chihindu. Zinatenga nthawi kuti ine ndi chibwenzi changa tifotokoze zimene tasankha. Tinavomera kusintha zinthu zina zimene tinkaona kuti sizikhumudwitsa Yehova. Mwachitsanzo, tinasintha zakudya n’kusankha zimene iwowo amakonda komanso tinasankha kuti pasadzakhale nyimbo komanso kuvina, chifukwa zinali zosiyana ndi chikhalidwe chawo.”

18. Kodi mungatani kuti zinthu zidzayende bwino pa tsiku la ukwati wanu? (1 Akorinto 14:40) (Onaninso chithunzi.)

18 Muzikonzekera mokwanira. Kukonzekereratu kungakuthandizeni kuti musadzakhale ndi nkhawa pa tsiku la ukwati. (Werengani 1 Akorinto 14:40.) M’bale Wayne wa ku Taiwan, anati: “Kutatsala masiku ochepa kuti ukwati wathu uchitike, tinakumana ndi anthu amene anadzipereka kuti atithandize. Tinakambirana zomwe tinakonza komanso tinayeserera mbali zina zimene zidzachitike pa ukwatipo, kuti titsimikizire kuti chilichonse chidzayenda bwino.” Pofuna kulemekeza anthu amene mwawaitana, mungachite bwino kudzachita zinthu m’nthawi yake.

Mwamuna ndi mkazi omwe ali pa chibwenzi akukambirana zomwe akonza zokhudza ukwati wawo ndi anzawo omwe awapempha kuti adzawathandize. M’bale akuwaonetsa mapulani a mmene anthu adzakhalire kumalo ochitira mwambo wa ukwati.

Kukonzekera bwino kungathandize kuti zinthu zidzayende bwino pa tsiku la ukwati (Onani ndime 18)


19. Kodi mungatani kuti mudzaonetsetse kuti zinthu zikuyenda bwino pa nthawi imene phwando lili mkati?

19 Mungapewe mavuto ambiri ngati mutaoneratu mavuto amene angadzakhalepo komanso mmene mungawathetsere. (Miy. 22:3) Mwachitsanzo, ngati kwanuko anthu amakonda kupita ku ukwati asanaitanidwe, mungakonze zoti mudzachite kuti zimenezi zisadzachitike. Muzionetsetsa kuti wachibale aliyense yemwe si wa Mboni akudziwa zomwe mwakonza kuti zidzachitike komanso zimene mumakhulupirira pa miyambo ina yokhudza ukwati. Mungakambirane nawo nkhani yakuti “Kodi pa Ukwati wa Mboni za Yehova Pamachitika Zotani?” imene ili pa webusaiti ya jw.org. Kuti ukwati wanu udzayende bwino, mungapemphe m’bale wolimba mwauzimu kuti adzakhale ‘woyang’anira phwando.’ (Yoh. 2:8) Ngati mutamufotokozera momveka bwino mapulani anu, angakuthandizeni kuti pa tsikuli zinthu zidzachitike mwaulemu komanso mmene munakonzera.

20. Kodi amene akufuna kukwatirana ayenera kukumbukira chiyani zokhudza tsiku la ukwati wawo?

20 Mungamade nkhawa mukaganizira zonse zimene zimafunika pokonzekera ukwati. Komabe muzikumbukira kuti phwando la ukwati limakhala tsiku limodzi basi. Chimangokhala chiyambi cha moyo wosangalatsa umene mudzakhale mukutumikira Yehova limodzi. Ndiye chitani zonse zimene mungathe kuti ukwati wanu udzakhale wosalira zambiri komanso wolemekezeka. Muzidalira Yehova. Iye angakuthandizeni kukonzekera ukwati umene muzidzati mukakumbukira, muzidzasangalala kwambiri popanda kunong’oneza bondo.—Sal. 37:​3, 4.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’chifukwa chiyani amene akufuna kukwatirana ayenera kudzalemekeza Yehova pa tsiku la ukwati wawo?

  • Kodi amene akufuna kukwatirana angatani kuti tsiku la ukwati wawo lidzakhale losangalatsa komanso lolemekezeka?

  • N’chifukwa chiyani amene akufuna kukwatirana zinthu zingawayendere bwino atakonza zoti ukwati wawo udzakhale wosalira zambiri?

NYIMBO NA. 107 Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

a MATANTHAUZO A MAWU ENA: M’zikhalidwe zambiri, pa tsiku la ukwati pamakhala mwambo umene anthu amene akukwatirana amalumbira pamaso pa Mulungu. Pambuyo pake pamakhala phwando la ukwati. M’madera amene sakhala ndi mwambo kapena phwando la ukwati, anthu amene akufuna kukwatirana angachite bwino kutsatira mfundo za m’Baibulo pa tsiku la ukwati wawo.

b Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene Akhristu amaonera malamulo a boma okhudza ukwati, onani nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2006, yamutu wakuti “Ukwati Wolemekezeka kwa Mulungu ndi kwa Anthu.”

c Onerani vidiyo imene ili pa jw.org yamutu wakuti, Kodi Padzakhale Mowa Kapena Ayi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena