MARCH 9-15, 2026
NYIMBO NA. 45 Zimene Ndimaganizira Mozama
N’zotheka Kulimbana ndi Maganizo Ofooketsa
“Munthu womvetsa chisoni ine!”—AROMA 7:24.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona zimene tingachite kuti tikwanitse kulimbana ndi maganizo ofooketsa.
1-2. Kodi nthawi zina mtumwi Paulo ankamva bwanji, nanga ifeyo timafanana naye m’njira ziti? (Aroma 7:21-24)
N’CHIYANI chimabwera m’maganizo mwanu mukaganizira za mtumwi Paulo? Kodi mumaganizira za mmishonale wolimba mtima, mphunzitsi waluso kapena munthu amene analemba mabuku ambiri m’Baibulo? Zimenezitu n’zolondola. Komatu nthawi zina ankakhumudwa komanso ankakhala ndi nkhawa. Mofanana ndi ambiri a ife, nthawi zinanso ankalimbana ndi maganizo ofooketsa.
2 Werengani Aroma 7:21-24. M’kalata yopita kwa Akhristu a ku Roma, Paulo anafotokoza mmene ankamvera ndipo zomwe anafotokozazi n’zimenenso zimatichitikira. Ngakhale kuti anali Mkhristu wokhulupirika, pali zinthu zina zimene ankalimbana nazo. Iye ankafunitsitsa kumachita zimene Mulungu amafuna. Koma ankalimbananso ndi kamtima kofuna kuchita zoipa. Kuwonjezera pamenepa, nthawi zina Paulo ankavutikanso ndi maganizo ofooketsa a zimene ankachita m’mbuyo komanso vuto lina lomwe silinathe.
3. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani? (Onaninso “Tanthauzo la Mawu Ena.”)
3 Ngakhale kuti Paulo ankalimbana ndi zinthu zofooketsa, sanalole kuti azingokhalira kuganizira zimenezo.a Munkhaniyi, tikambirana mafunso awa: N’chiyani chinkapangitsa Paulo kuti nthawi zina azidziona kuti ndi munthu “womvetsa chisoni”? Kodi anatani kuti alimbane ndi maganizo ofooketsa? Nanga ifeyo tingatani kuti tikwanitse kulimbana ndi maganizo ofooketsa?
N’CHIYANI CHINAPANGITSA PAULO KUKHALA NDI MAGANIZO OFOOKETSA?
4. Kodi n’chiyani chinkamupangitsa Paulo kuti akhale ndi maganizo ofooketsa?
4 Zinthu zomwe ankachita m’mbuyo. Asanakhale Mkhristu, Paulo amene poyamba ankadziwika kuti Saulo, anachita zinthu zimene pambuyo pake anadzanong’oneza nazo bondo. Mwachitsanzo, iye analipo pamene Sitefano ankaponyedwa miyala ndipo anavomereza zoti aphedwe. (Mac. 7:58; 8:1) Komanso ankatsogolera pozunza Akhristu mwankhanza.—Mac. 8:3; 26:9-11.
5. Kodi Paulo ankamva bwanji akaganizira zimene anachita m’mbuyo?
5 Atakhala Mkhristu, nthawi zina Paulo ankadziimba mlandu chifukwa cha zimene anachita m’mbuyo. Pamene zaka zinkapita, ayenera kuti ankavutika kwambiri akakumbukira kuti ankazunza Akhristu mwankhanza. M’kalata yoyamba imene analembera Akhristu a ku Korinto cha m’ma 55 C.E., ananena kuti: “Si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” (1 Akor. 15:9) Patapita zaka pafupifupi 5, pamene ankalemba kalata yopita kwa Aefeso, iye ananena kuti ndi ‘wamngʼono poyerekeza ndi wamngʼono kwambiri pa oyera onse.’ (Aef. 3:8) Pamene ankalembera kalata Timoteyo, Paulo ananena kuti poyamba anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) Kodi mukuganiza kuti Paulo ayenera kuti ankamva bwanji pamene ankayendera mipingo n’kumakumana ndi anthu amene poyamba ankawazunza kapena achibale awo?
6. Kodi chinanso n’chiyani chimene chinkamupangitsa Paulo kuti azikhala ndi nkhawa? (Onaninso mawu a m’munsi.)
6 Minga m’thupi. Paulo anayerekezera zinthu zinazake zimene zinkamudetsa nkhawa kwambiri ndi “minga mʼthupi.” (2 Akor. 12:7) Mtumwiyu sananene chimene chinkamupangitsa kuti azimva kupweteka kwambiri. N’kutheka kuti anali matenda kapena vuto lina limene linkamuchititsa kuti azikhala ndi nkhawa.b
7. N’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti Paulo azichita zinthu zoyenera nthawi zonse? (Aroma 7:18, 19)
7 Zimene ankalakwitsa. Paulo ankavutika chifukwa cha zimene ankalakwitsa. (Werengani Aroma 7:18, 19.) Ngakhale kuti ankafuna kumachita zoyenera, ankavutika kuchita zimenezi chifukwa choti sanali wangwiro. Iye anavomereza kuti anali pankhondo yolimbana ndi zinthu zoipa zimene thupi lake linkalakalaka ndi zinthu zabwino zimene ankafuna kumachita. Komabe ankayesetsa kuchita zoyenera. (1 Akor. 9:27) Iye ayenera kuti ankakhumudwa kwambiri akachitanso zinthu zimene anachita khama kuti azisiye.
KODI PAULO ANKACHITA CHIYANI KUTI ALIMBANE NDI MAGANIZO OFOOKETSA?
8. Kodi ndi zinthu ziti zimene Paulo ankachita zomwe zinamuthandiza polimbana ndi zimene ankalakwitsa?
8 M’makalata amene analemba, Paulo anasonyeza mmene mzimu woyera unathandizira iyeyo komanso Akhristu anzake kulimbana ndi zinthu zoipa zimene ankalakalaka. (Aroma 8:13; Agal. 5:16, 17) Nthawi zambiri ankatchula za makhalidwe komanso zilakolako zoipa zimene Akhristu ayenera kulimbana nazo. (Agal. 5:19-21, 26) N’zosachita kufunsa kuti Paulo ankaganizira zimene ankalakwitsa, kufufuza malangizo m’Malemba komanso kupeza njira zomuthandiza kulimbana ndi zimene ankalakwitsazo. N’zodziwikiratu kuti nayenso ankagwiritsa ntchito malangizo amene anapereka kwa anthu ena.
9-10. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti alimbane ndi maganizo ofooketsa? (Aefeso 1:7) (Onaninso chithunzi.)
9 Ngakhale kuti nthawi zina Paulo ankafooka, panali zinthu zambiri zimene zinkamupangitsa kuti azisangalalabe. Mwachitsanzo, ankasangalala akamva malipoti abwino okhudza mmene mipingo ikuyendera. (2 Akor. 7:6, 7) Ankasangalalanso chifukwa chogwirizana ndi Akhristu anzake. (2 Tim. 1:4) Komanso ankadziwa kuti Yehova akusangalala naye. Paulo ankasangalala chifukwa choti ankatumikira Mulungu ndi “chikumbumtima choyera.” (2 Tim. 1:3) Ngakhale pamene anamangidwa ku Roma, iye analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘azisangalala chifukwa cha Ambuye.’ (Afil. 4:4) Tikamawerenga zimene Paulo analemba, timaona kuti sikuti iye ankangoganizira zinthu zimene zinkamufooketsa. N’zoonekeratu kuti akayamba kuganizira zinthu zofooketsa, nthawi yomweyo ankasintha n’kuyamba kuganizira zinthu zabwino.
10 Paulo anakwanitsanso kulimbana ndi maganizo ofooketsa chifukwa ankakhulupirira kuti dipo ndi mphatso imene Mulungu anamupatsa iyeyo mwachindunji. (Agal. 2:20; werengani Aefeso 1:7.) Choncho sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova amakhululuka kudzera mwa Yesu Khristu. (Aroma 7:24, 25) Ngakhale kuti anachita zinthu zoipa komanso ankalakwitsa zinthu zina, Paulo anakwanitsa kuchita “utumiki wopatulika kwa Mulungu” mosangalala.—Aheb. 9:12-14.
Ngakhale kuti nthawi zina Paulo ankavutika maganizo chifukwa cha zimene anachita m’mbuyo, iye anatha kulimbana ndi maganizo ofooketsa chifukwa choganizira mozama zokhudza dipo (Onani ndime 9 ndi 10)
11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chitsanzo cha Paulo n’cholimbikitsa kwa ife?
11 Mofanana ndi Paulo, tingamamve kuti nthawi zonse tili pa nkhondo yolimbana ndi vuto linalake, mwina lokhuza zimene timaganiza, kuchita kapenanso kulankhula. N’kutheka kuti ifenso tingafike ponena kuti, ‘Munthu womvetsa chisoni ine!’ Ponena za vuto limene akulimbana nalo, mlongo wina wazaka za m’ma 20 dzina lake Elizac ananena kuti: “Ndimalimbikitsidwa ndikaganizira zimene zinkachitikira Paulo. Ndimamvako bwino kudziwa kuti si ine ndekha amene ndikufunika kusintha. Zimenezi zimandikumbutsa kuti Yehova amadziwa zimene anthu ake akukumana nazo.” Ndiye kodi tingatani kuti mofanana ndi Paulo tizikhalabe ndi chikumbumtima choyera n’kumasangalala ngakhale kuti nthawi zina tingamavutike ndi maganizo ofooketsa?
KODI TINGATANI KUTI TIZIKWANITSA KULIMBANA NDI MAGANIZO OFOOKETSA?
12. Kodi kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse kumatithandiza bwanji kulimbana ndi maganizo ofooketsa?
12 Muzichita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse. Tikamachita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, zimatithandiza kuti tiziganizira zinthu zabwino. Tingayerekezere zimenezi ndi kuchita zinthu zomwe zingatithandize kukhala ndi thanzi labwino. Tikamadya zakudya zabwino, kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kugona mokwanira timakhala ndi thanzi labwino. Mofanana ndi zimenezi, tonsefe timamva bwino tikamawerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kukonzekera, kupezeka komanso kutenga nawo mbali pamisonkhano ndiponso kugwira nawo ntchito yolalikira. Zimenezi zimatithandiza kuti tizikwanitsa kulimbana ndi maganizo ofooketsa.—Aroma 12:11, 12.
13-14. Kodi kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse kwathandiza bwanji Akhristu ena okhulupirika?
13 Taganizirani za John yemwe anapezeka ndi khansa ali ndi zaka 39. Poyamba ankavutika kwambiri ndi nkhawa. Iye ankadzifunsa kuti: ‘Ndingapezeke bwanji ndi khansa ndili ndi zaka zochepa chonchi?’ Pa nthawiyo, mwana wake anali ndi zaka zitatu zokha. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kulimbana ndi nkhawa zomwe anali nazo? Iye anati: “Ngakhale kuti ndinkakhala wotopa, ndinkaonetsetsa kuti banja lathu likuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse. Tinkapita kumisonkhano yonse, kulowa mu utumiki mlungu uliwonse komanso tinkachita kulambira kwa pabanja nthawi zonse ngakhale pa nthawi imene zinali zovuta kuchita zimenezo.” Poganizira zimene zinkachitika, John ananenanso kuti: “Poyamba umakhala ndi nkhawa kwambiri. Koma kenako umayamba kuona Yehova akukupatsa mphamvu komanso kukusonyeza chikondi. Yehova angakupatseni mphamvu ngati mmenenso anachitira ndi ine.”
14 Eliza yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Nthawi iliyonse imene ndapita kumisonkhano komanso kuphunzira Baibulo pandekha, zimandikumbutsa kuti Yehova amandimvetsera komanso amandikonda kwambiri. Zimenezi zimandithandiza kukhala wosangalala.” Ponena za iyeyo komanso mkazi wake Diane, Nolan yemwe ndi woyang’anira dera wa ku Africa, ananena kuti: “Nthawi zonse timachita zinthu zokhudza kulambira ngakhale pamene takumana ndi zinthu zokhumudwitsa. Zimachita kuonekeratu kuti nthawi zonse Yehova amatithandiza kukhala ndi maganizo oyenera. Timayesetsa kukumbukira kuti Yehova adzatithandiza komanso kutidalitsa. Sitidziwa mmene adzachitire zimenezi koma timadziwa kuti adzazichita ndithu.”
15. Kodi tingafunikenso kuchita chiyani kuti tikwanitse kulimbana ndi maganizo ofooketsa? Perekani chitsanzo.
15 Pali zinanso zomwe tingachite kuti tilimbane ndi maganizo ofooketsa. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti msana wayamba kukupwetekani. Mukhoza kuyamba kumvako bwino ngati mutamapeza nthawi yoyenda tsiku lililonse. Komabe kuti vutoli lithe, muyenera kuchita zambiri. Kuti mudziwe chomwe chayambitsa vutoli, mungafunike kufufuza komanso kukaonana ndi dokotala. Mofanana ndi zimenezi, tingafunike kufufuza m’Baibulo komanso m’mabuku athu ngakhalenso kulankhula ndi Mkhristu wolimba mwauzimu kuti tidziwe zimene tingachite polimbana ndi maganizo ofooketsa amene amativutitsa nthawi zambiri. Tsopano tiyeni tione zinthu zinanso zomwe zingatithandize.
16. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuzindikira zinthu zimene zikukuchititsani kukhala ndi nkhawa? (Salimo 139:1-4, 23, 24)
16 Tizipempha Yehova kuti atithandize kudziwa zimene zingathandize ifeyo patokha. Mfumu Davide ankadziwa kuti Yehova ankamudziwa bwino. Choncho anapempha Yehova kuti amuthandize kudziwa zinthu zimene zinkamuchititsa kuti ‘azida nkhawa.’ (Werengani Salimo 139:1-4, 23, 24.) Inunso mukhoza kupempha Yehova kuti akuthandizeni kudziwa chifukwa chake muli ndi maganizo ofooketsa komanso zimene mungachite kuti muthane nawo. Mukhozanso kudzifunsa mafunso ngati awa: ‘N’chiyani kwenikweni chimene chikuchititsa kuti ndizikhala ndi nkhawa? Kodi pali chinachake chimene chikuchititsa kuti ndiyambe kukhala ndi maganizo ofooketsa? Zinthu zofooketsa zikandibwerera m’maganizo, kodi ndimapitiriza kuziganizira kapena ndimasiya nthawi yomweyo?
17. Kodi mungaphunzire nkhani ziti zomwe zingakuthandizeni kuti muziganizira kwambiri zinthu zolimbikitsa? (Onaninso chithunzi.)
17 Muziphunzira Baibulo mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Ndi bwino kuti nthawi zina muziphunzira ena mwa makhalidwe a Yehova. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anapindula kwambiri chifukwa choganizira zokhudza dipo komanso mmene Yehova amatikhululukira. Inunso mukhoza kuchita chimodzimodzi. Muzigwiritsa ntchito Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani, Watch Tower Publications Index komanso zinthu zina zothandiza pophunzira za m’chilankhulo chanu, pofufuza nkhani zokhudza chifundo, kukhululuka komanso chikondi chokhulupirika cha Mulungu. Mukapeza nkhani zimene zingakuthandizeni, muzilemba mitu yake n’kuisunga penapake pomwe mukhoza kuiona mosavuta. Ndiye mukayamba kukhala ndi maganizo ofooketsa muziphunzira nkhanizo. Muziyesetsa kugwiritsa ntchito zimene mwawerenga mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu.—Afil. 4:8.
Muziphunzira nkhani zimene zingakuthandizeni kulimbana ndi maganizo ofooketsa (Onani ndime 17)
18. Kodi Akhristu ena anafufuza nkhani ziti zomwe zinawathandiza?
18 Eliza, yemwe tamutchula kale uja, anaphunzira nkhani yokhudza Yobu. Iye anati: “Zambiri mwa zomwe zinandichitikira ndi zomwenso zinachitikira Yobu. Iye anakumana ndi mayesero motsatizanatsatizana. Komabe pamene anali ndi nkhawa kwambiri, sanasiye kudalira Yehova ngakhale kuti sankadziwa chimene chinkayambitsa mavuto ake.” (Yobu 42:1-6) Diane yemwenso tamutchula kale uja ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga tikuphunzira buku la Yandikirani Yehova. Timayamikira kuti Yehova akutiumba ngati mmene woumba mbiya amachitira. M’malo moganizira kwambiri zimene timalakwitsa, timaganizira mmene Yehova akutiumbira kuti tikhale anthu abwino. Zimenezi zimathandiza kuti akhale Mnzathu wapamtima.”—Yes. 64:8.
TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA ADZATITHANDIZA KOMANSO KUTIDALITSA
19. Kodi nthawi zina tingamamve bwanji, koma kodi sitingakayikire za chiyani?
19 Ngakhale titamachita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse komanso kuphunzira Baibulo mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu, sitingasiyiretu kuganizira zinthu zofooketsa. Masiku ena tingamadzionebe kuti ndife omvetsa chisoni. Komabe mothandizidwa ndi Yehova, n’zotheka kusiya kuganizira zinthu zofooketsa. Tingakhale otsimikiza kuti nthawi zambiri tizisangalala chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso kudziwa kuti akusangalala ndi zimene tikuchita pomutumikira.
20. Kodi ndinu wotsimikiza mtima kuchita chiyani?
20 Tiyeni titsimikize mtima kuti tisalole mavuto athu, zomwe tinkachita m’mbuyo komanso zimene timalakwitsa kutilepheretsa kukhala osangalala. Yehova akhoza kutithandiza kuti tisiye kuganizira zofooketsa. (Sal. 143:10) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene tizidzangoganizira zinthu zabwino. Tsiku lililonse tizidzadzuka tilibe nkhawa n’kumatumikira Mulungu wathu Yehova mosangalala.
NYIMBO NA. 34 Kuchita Zinthu Mokhulupirika
a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu akuti “maganizo ofooketsa” akunena za kumva chisoni ndiponso nkhawa zomwe timakhala nazo nthawi zina. Sakutanthauza matenda ovutika maganizo omwe amafunika thandizo lachipatala.
b Zimene Paulo analemba zimasonyeza kuti anali ndi vuto la maso lomwe linkachititsa kuti azivutika kulemba makalata komanso kuchita utumiki wake. (Agal. 4:15; 6:11) Kapenanso mwina Paulo ankada nkhawa chifukwa cha zimene aphunzitsi abodza ankanena zokhudza iyeyo. (2 Akor. 10:10; 11:5, 13) Kaya Paulo ankada nkhawa pa zifukwa ziti, zimenezi zinkamuvutitsa maganizo.
c Mayina ena asinthidwa.