Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 January tsamba 2-7
  • Pitirizani Kukwaniritsa ‘Zosowa Zanu Zauzimu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kukwaniritsa ‘Zosowa Zanu Zauzimu’
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MAKHALIDWE ATATU OFUNIKA KWAMBIRI AMENE TIMAFUNIKA KUKHALA NAWO
  • MUZITSANZIRA PETULO POPITIRIZA KUDYA CHAKUDYA CHAUZIMU
  • MUZITSANZIRA PAULO POPITIRIZA KUVALA UMUNTHU WATSOPANO
  • MUZITSANZIRA DAVIDE POPITIRIZA KUKHALA M’MALO OTETEZEKA AUZIMU
  • PITIRIZANI KUKWANIRITSA ZOSOWA ZANU ZAUZIMU
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Tizitsanzira Mmene Yehova ndi Yesu Amaganizira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woyang’anira Dera wa 2025-2026
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 January tsamba 2-7

MARCH 2-8, 2026

NYIMBO NA. 97 Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala ndi Moyo

Pitirizani Kukwaniritsa ‘Zosowa Zanu Zauzimu’

LEMBA LA CHAKA CHA 2026: “Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—MAT. 5:3.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zomwe tingachite kuti tipitirize kupindula ndi chakudya chauzimu, zovala zauzimu komanso malo otetezeka auzimu amene Yehova amatipatsa.

1. Kodi ndi zinthu ziti zimene anthufe timafunikira? (Mateyu 5:3)

YEHOVA amadziwa zimene anthufe timafunikira. Mwachitsanzo, kuti tipitirizebe kukhala ndi moyo timafunikira chakudya, zovala komanso malo okhala. Ngati tilibe chimodzi mwa zinthu zimenezi ngakhale kwa nthawi yochepa, moyo umakhala wovuta kwambiri. Kuwonjezera pa zimenezi, Yehova anatilenganso ndi mtima woti tizifunitsitsa kukwaniritsa zosowa zathu zauzimu. (Werengani Mateyu 5:3.) Ngati tikufuna kuti tizikhaladi osangalala, timafunika kuzindikira zosowa zathu zauzimu n’kumapitiriza kuzikwaniritsa.

2. Kodi ‘kuzindikira zosowa zauzimu’ kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

2 Kodi ‘kuzindikira zosowa zathu zauzimu’ kumatanthauza chiyani? Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti ‘zosowa zauzimu’ amanena za munthu wopemphapempha. Mawuwa akutipangitsa kuganiza za munthu wosauka kwambiri amene wavala zovala zong’ambikang’ambika, atakhala pansi m’mbali mwa msewu m’tauni. Iye wafookeratu chifukwa chosowa zakudya, anthu akumusala chifukwa cha mmene akuonekera, tsiku lonse amakhala padzuwa ndipo amakhala akuzizidwa usiku wonse. Munthuyu akudziwa kuti akufunika kuthandizidwa kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino pa moyo wake. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene amazindikira zosowa zake zauzimu, kapena kuti amene amapemphapempha mzimu woyera. Iye amadziwa kuti amafunikira kuthandizidwa ndi Mulungu kuti zinthu zizimuyendera bwino. Choncho amayesetsa kugwiritsa ntchito chakudya chochuluka chauzimu chimene Yehova amapereka kwa anthu amene amamukonda.

3. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani?

3 Munkhaniyi, choyamba tikambirana zimene tikuphunzirapo kwa mayi wa ku Foinike amene anapempha Yesu kuti amuthandize. Nkhani ya mayiyu itithandiza kuona makhalidwe atatu amene anthu omwe amazindikira zosowa zawo zauzimu amafunika kukhala nawo. Kenako tikambirana chitsanzo cha mtumwi Petulo, mtumwi Paulo komanso cha Mfumu Davide, omwe anali amuna olimba mwauzimu.

MAKHALIDWE ATATU OFUNIKA KWAMBIRI AMENE TIMAFUNIKA KUKHALA NAWO

4. Kodi mayi wa ku Foinike ankafuna kuti Yesu amuchitire chiyani?

4 Tsiku lina mayi wina wa ku Foinike anabwera kwa Yesu. Mwana wake wamkazi anagwidwa ndi ‘chiwanda chimene chinkamuzunza mwankhanza.’ (Mat. 15:​21-28) Mayiyo anagwada n’kupempha Yesu kuti amuthandize. Pamene ankalankhula ndi Yesu anasonyeza makhalidwe abwino kwambiri. Tiyeni tikambirane ena mwa makhalidwewa.

5. Kodi mayiyu anasonyeza makhalidwe ati, nanga Yesu anamuthandiza bwanji? (Onaninso chithunzi.)

5 Mayi wa ku Foinikeyu anali wodzichepetsa kwambiri. Tikutero chifukwa sanakhumudwe Yesu atagwiritsa ntchito chitsanzo chomwe chinkaoneka ngati chikumuyerekezera ndi tiagalu, tomwe nthawi zina anthu amene si Ayuda ankaweta panyumba pawo. Mukaganizira zimene Yesu analankhulazi, kodi mukanakhala inuyo mukanatani? Kodi mukanaona kuti wakunyozani n’kungochokapo osapitiriza kumupempha kuti akuthandizeni? Zimenezi si zomwe mayiyu anachita. Iye anasonyeza kudzichepetsa komanso anali ndi mtima wofunitsitsa kuthandizidwa. Zimenezi zinaonekera bwino pamene anapitirizabe kupempha Yesu kuti amuthandize. Iye anachita zimenezi chifukwa ankakhulupirira kwambiri Yesu. Yesu ataona kuti mayiyu ali ndi chikhulupiriro cholimba anaganiza zoti amuthandize. Ngakhale kuti pa nthawiyi Yesu anali atangonena kuti anabwera kudzathandiza “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli,” iye anatulutsa chiwanda chimene chinagwira mwana wa mayiyo ngakhale kuti sanali Myuda.

Mayi wa ku Foinike wagwada ndipo akupempha Yesu kuti amuthandize. Yesu ndi ophunzira ake atatu akumumvetsera ndipo pambali pawo pali tebulo la zakudya.

Kuti athandizidwe, mayi wa ku Foinike ankafunika kukhala wodzichepetsa, kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuthandizidwa komanso chikhulupiriro (Onani ndime 5)


6. Kodi nkhani ya mayi wa ku Foinike ikutiphunzitsa chiyani?

6 Kuti ifenso tikwaniritse zosowa zathu zauzimu, timafunika kukhala odzichepetsa, kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuthandizidwa komanso chikhulupiriro cholimba. Anthu odzichepetsa okha ndi amene amapitirizabe kupempha Mulungu kuti awathandize. Tizikhulupiriranso kwambiri Khristu Yesu komanso anthu amene akuwagwiritsa ntchito potsogolera ophunzira ake. (Mat. 24:​45-47) Yehova ndi Yesu amasangalala kuthandiza anthu amakhalidwe amenewa kukwaniritsa zosowa zawo zauzimu. (Yerekezerani ndi Yakobo 1:​5-7.) Tsopano tiyeni tikambirane njira zimene Yehova amatipatsira chakudya chauzimu, zovala zauzimu komanso malo otetezeka. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mtumwi Petulo, mtumwi Paulo komanso Mfumu Davide, tiona zimene tingachite kuti tizitha kupeza zinthu zofunikazi.

MUZITSANZIRA PETULO POPITIRIZA KUDYA CHAKUDYA CHAUZIMU

7. Kodi Yesu analamula Petulo kuti achite chiyani, nanga kodi Petuloyo ankafunikanso kuchita chiyani? Fotokozani. (Aheberi 5:14–6:1)

7 Tiyeni tiganizire chitsanzo cha mtumwi Petulo. Iye anali mmodzi mwa Ayuda oyambirira omwe anazindikira kuti Yesu ndi Mesiya, yemwe Yehova ankamugwiritsa ntchito kudyetsa anthu ake ‘mawu othandiza kuti adzapeze moyo wosatha.’ (Yoh. 6:​66-68) Yesu asanabwerere kumwamba, analamula Petulo kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:17) Petulo anamvera zimene Yesu anamulamula ndipo Yehova anamugwiritsa ntchito kulemba makalata awiri amene anadzakhala mbali ya Baibulo. Komabe Petulo nayenso ankafunika kuti payekha azidzidyetsa mwauzimu. Iye ankawerenga komanso kuphunzira makalata ouziridwa amene Paulo anali atalemba kale. Petulo anavomereza kuti zina mwa zimene Paulo analemba zinali “zovuta kuzimvetsa.” (2 Pet. 3:​15, 16) Koma iye sanagwe ulesi. Ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito “chakudya chotafuna” chimene Paulo anauziridwa kulemba m’makalata ake.—Werengani Aheberi 5:14–6:1.

8. Kodi Petulo anatani atalandira malangizo atsopano kuchokera kwa Yehova?

8 Petulo anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova pomvera malangizo atsopano amene anapatsidwa. Mwachitsanzo, ali mumzinda wa Yopa anaona masomphenya, mngelo akumuuza kuti aphe komanso adye nyama zimene mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, zinali zodetsedwa. Kwa Ayuda malangizo amenewa anali achilendo. Poyamba Petulo anayankha kuti: “Ayi Ambuye, ine sindinadyepo chinthu chodetsedwa ndiponso chonyansa chilichonse.” Kenako anauzidwa kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti nʼzodetsedwa.” (Mac. 10:​9-15) Petulo anamvetsa mfundo yake. Tikutero chifukwa atangomaliza kuona masomphenyawo, amuna atatu omwe anatumidwa ndi Koneliyo, yemwe sanali Myuda, anafika ndipo anamuitana kuti apite kunyumba ya mbuye wawo. Asanaone masomphenyawo, Petulo sakanalola kuti akalowe m’nyumba ya munthu yemwe si Myuda. Ayuda ankaona kuti anthu amitundu ina ndi odetsedwa. (Mac. 10:​28, 29) Koma nthawi yomweyo Petulo anavomera malangizo atsopano amene Yehova anamupatsa. (Miy. 4:18) Iye analalikira kwa Koneliyo ndi anthu a m’banja lake ndipo anasangalala kuwaona akumvetsera uthenga wa choonadi, akulandira mzimu woyera komanso kubatizidwa.—Mac. 10:​44-48.

9. Kodi tingapindule m’njira ziwiri ziti tikamalakalaka kwambiri chakudya chotafuna chauzimu?

9 Mofanana ndi Petulo, nthawi zonse timafunika kumamwa mkaka, kapena kuti kudziwa mfundo zoyambirira za choonadi za m’Mawu a Mulungu. Timafunikanso kukhala ndi mtima wolakalaka chakudya chotafuna, chomwe ndi mfundo za choonadi zimene zikhoza kukhala zovuta kwambiri kuzimvetsa. Tizipeza nthawi yokwanira komanso tizichita khama kuphunzira mfundo zozama ndipo kuchita zimenezi n’kothandiza kwambiri. Choyamba, timaphunzira zinthu zokhudza Yehova zomwe zimatichititsa kuti tizimukonda komanso kumulemekeza kwambiri. Chachiwiri, zimatilimbikitsa kuti tizifuna kuuza ena zokhudza Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wochititsa chidwi. (Aroma 11:33; Chiv. 4:11) Chitsanzo cha Petulo chikutiphunzitsanso chinthu china. Pakakhala kusintha mmene timamvera mfundo inayake ya m’Mawu a Mulungu, ifenso tizisintha mofulumira n’kuyamba kutsatira mfundo yatsopanoyo. Tikamachita zimenezi timakhala tikupitiriza kudyetsedwa bwino mwauzimu ndipo Yehova amapitiriza kutigwiritsa ntchito.

MUZITSANZIRA PAULO POPITIRIZA KUVALA UMUNTHU WATSOPANO

10. Kodi kuvala umunthu watsopano kumaphatikizapo chiyani? (Akolose 3:​8-10)

10 Kuti tizisangalatsa Mulungu timafunikanso kugwiritsa ntchito chinthu china chimene Yehova amatipatsa, chomwe ndi chovala chauzimu. Kodi tikutanthauza chiyani? Mtumwi Paulo analemba kuti tiyenera ‘kuvula umunthu wakale n’kuvala umunthu watsopano.’ (Werengani Akolose 3:​8-10.) Zimenezi zimafunika nthawi komanso khama. Taganizirani chitsanzo cha Paulo. Kuyambira ali mwana ankayesetsa kuti azisangalatsa Mulungu. (Agal. 1:14; Afil. 3:​4, 5) Koma sankadziwa zinthu zolondola zokhudza cholinga cha Mulungu komanso njira yoyenera yomulambirira. Chifukwa chakuti sankadziwa choonadi chokhudza zimene Yesu ankaphunzitsa komanso anali wonyada, iye anali “wachipongwe” ndipo analibe makhalidwe abwino.—1 Tim. 1:13.

11. Kodi ndi khalidwe liti limene Paulo ankafunika kuchita khama kuti alisinthe? Fotokozani.

11 Asanakhale Mkhristu, Paulo sankachedwa kupsa mtima. Nkhani ya m’buku la Machitidwe imanena kuti Paulo anakwiya kwambiri moti ‘ankaopseza komanso ankafunitsitsa kupha’ ophunzira a Yesu. (Mac. 9:1) Koma atakhala Mkhristu n’zosakayikitsa kuti anachita khama kuti avule umunthu wake wakalewu. (Aef. 4:​22, 31) Ngakhale zinali choncho, pa nthawi ina Paulo ndi Baranaba anasemphana maganizo moti “anakangana koopsa.” (Mac. 15:​37-39) Limeneli ndi vuto limene Paulo anali nalo koma anapitirizabe kulimbana nalo. Iye anapitiriza ‘kumenya thupi lake,’ kapena kuti kulimbana ndi vuto lakeli n’cholinga choti azisangalatsa Yehova.—1 Akor. 9:27.

12. N’chiyani chinathandiza Paulo kuti akwanitse kuvula umunthu wake wakale?

12 Paulo anakwanitsa kuvula umunthu wake wakale n’kuvala umunthu watsopano chifukwa sankadalira mphamvu zake. (Afil. 4:13) Mofanana ndi Petulo, Paulo ankadalira “mphamvu imene Mulungu amapereka.” (1 Pet. 4:11) Ngakhale zinali choncho, nthawi zina iye ankadzimva ngati wolephera. Komabe kuganizira zinthu zabwino zimene Atate wake wakumwamba anamuchitira kunkamulimbikitsa kuti asafooke koma apitirize kulimbana ndi vuto lakeli.—Aroma 7:​21-25.

13. Kodi tingamutsanzire bwanji Paulo?

13 Kaya tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tingatsanzire Paulo popitiriza kuchita khama kuvula umunthu wathu wakale n’kuvala umunthu watsopano umene uli ngati chovala chauzimu chimene Mulungu amapereka. Ngati tabwerezanso khalidwe linalake limene tinayesetsa kulisintha, mwachitsanzo kusachedwa kupsa mtima kapena kusalankhula bwino, tisamadzione ngati ndife olephera. M’malomwake, tiziyesetsa kukwanitsa cholinga chathu chosintha mmene timaganizira komanso mmene timachitira zinthu. (Aroma 12:​1, 2; Aef. 4:24) Komabe pochita zimenezi tizikumbukira mfundo yofunika iyi: Mosiyana ndi zovala zenizeni zimene zikhoza kusinthidwa kuti zitikwane, ifeyo ndi amene timafunika kusintha zinthu zina ndi zina kuti tikwanitse kuvala chovala chauzimu chimene Yehova amapereka. Ndipotu m’pomveka kuti ifeyo ndi amene timafunika kusintha umunthu wathu kuti tikwanitse kuchita zimene Mulungu amafuna.

MUZITSANZIRA DAVIDE POPITIRIZA KUKHALA M’MALO OTETEZEKA AUZIMU

14-15. Kodi Yehova amapereka bwanji malo otetezeka auzimu kwa anthu ake? (Salimo 27:5) (Onaninso chithunzi chapachikuto.)

14 Kuwonjezera pa chakudya komanso zovala zauzimu, kuti tizisangalala zenizeni timafunikiranso malo otetezeka auzimu. Kodi malo amenewa ndi ati, nanga tingatani kuti tipitirizebe kukhala m’malo otetezekawa?

15 Mfumu Davide anafotokoza za malo otetezeka auzimu amene Yehova amapereka. (Werengani Salimo 27:5.) Yehova amateteza anthu ake kwa aliyense kapena chilichonse chimene chingapangitse kuti asiye kumukhulupirira. Ndiye kodi Yehova amatiteteza bwanji masiku ano? Iye amatilonjeza kuti chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chitivulaze sichidzapambana. (Sal. 34:7; Yes. 54:17) N’zoona kuti Satana ndi ziwanda zake ndi amphamvu, koma sangatiwononge mpaka kalekale. Ngakhale atawononga moyo wathu, Yehova akutilonjeza kuti adzatipatsanso moyo wina potiukitsa. (1 Akor. 15:​55-57; Chiv. 21:​3, 4) Iye amatithandizanso kuti tithe kulimbana ndi nkhawa zomwe zingatipangitse kusiya kumutumikira. (Miy. 12:25; Mat. 6:​27-29) Kuwonjezera pamenepa, Atate wathu wachikondi anatipatsa banja lauzimu lomwe limatithandiza komanso akulu amene amatiweta mwachikondi. (Yes. 32:​1, 2) Tikapita kumisonkhano timakaphunzira zimene tingachite kuti Yehova azitithandiza komanso kutiteteza.—Aheb. 10:​24, 25.

Mlongo waimika dzanja kuti ayankhe pa Phunziro la “Nsanja ya Olonda.” Abale ndi alongo ena nawonso aimika manja awo.

Mlongo akufuna kuthandizidwa ndi Yehova popezeka pamisonkhano ya mpingo limodzi ndi abale ndi alongo (Onani ndime 14-15)


16. Kodi Yehova anateteza Davide m’njira ziti?

16 Pamene Davide ankamvera Yehova, iye ankamuteteza ku mavuto omwe anthu amene amachita machimo mwadala amakumana nawo. (Yerekezerani ndi Miyambo 5:​1, 2.) Koma Davide atanyalanyaza mfundo za Mulungu, Yehova sanamuteteze ku zotsatira za zochita zakezo. (2 Sam. 12:​9, 10) Nanga bwanji pa nthawi imene Davide ankavutika chifukwa cha zoipa zimene anthu ena ankamuchitira? Iye anatulira Yehova nkhawa zake zonse ndipo Yehovayo anamulimbikitsa pomutsimikizira kuti amamukonda komanso kuti amusamalira.—Sal. 23:​1-6.

17. Kodi tingamutsanzire bwanji Davide?

17 Tingamutsanzire Davide pofufuza malangizo a Yehova tikafuna kusankha zochita. Timazindikiranso kuti nthawi zina tikhoza kukumana ndi mavuto, osati chifukwa chakuti Yehova walephera kutiteteza, koma chifukwa choti tasankha zinthu molakwika. (Agal. 6:​7, 8) Tikakumana ndi mavuto oyambitsidwa ndi anthu ena timamutulira Yehova nkhawa zathu m’pemphero, n’kumakhulupirira kuti ateteza mtima komanso maganizo athu.—Afil. 4:​6, 7.

PITIRIZANI KUKWANIRITSA ZOSOWA ZANU ZAUZIMU

18. Kodi ndi vuto liti limene timakumana nalo, nanga tingatani kuti tipitirizebe kukwaniritsa zosowa zathu zauzimu? (Onaninso zithunzi.)

18 Lemba la chaka cha 2026 likuti: “Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” Zimenezitu ndi zoona makamaka panopa kuposa kale lonse. Tikutero chifukwa m’dzikoli muli anthu ambiri osasangalala amene savomereza kuti ali ndi zosowa zauzimu kapenanso omwe amayesa kukwaniritsa zosowa zawo zauzimu pogwiritsa ntchito chipembedzo chabodza kapena nzeru za anthu. Tisamalole kuti kaganizidwe kameneka katisokoneze. Tingachite zimenezi podzidyetsa mokwanira chakudya chauzimu chimene Yehova amapereka, kuvala umunthu watsopano komanso kufunafuna malo otetezeka amene Yehova amatipatsa.

Zithunzi: Mlongo yemwe tamuona pachithunzi choyamba uja akupitiriza kukwaniritsa zosowa zake zauzimu. 1. Iye akuphunzira nkhani yophunzira mu “Nsanja ya Olonda.” 2. Wapita kukapereka chakudya kwa banja lina limene lili kunyumba kwawo. M’bale wakhala pampando, mutu wake aumanga ndi bandeji komanso pamkono pake pali dilipi ya madzi. 3. Iye akumvetsera mwatcheru pamene abale awiri amuyendera kukamulimbikitsa.

Timafunika kupitiriza kupeza chakudya chauzimu, zovala zauzimu komanso malo otetezeka auzimu (Onani ndime 18)a

KODI TINGATANI KUTI TIZIPINDULA NDI ZIMENE YEHOVA AMATIPATSA . . .

  • chakudya chauzimu?

  • zovala zauzimu?

  • malo otetezeka auzimu?

NYIMBO NA. 162 Zosowa Zanga Zauzimu

a MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo uja chinthuzi choyamba uja akudya chakudya chauzimu pophunzira Nsanja ya Olonda, pochitira ena zinthu mokoma mtima monga mbali ya kuvala umunthu watsopano komanso akupempha thandizo kwa akulu omwe akumuthandiza mwachikondi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena