UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani Mmisili Waluso
Kalipentala waluso amadziŵa bwino moseŵenzetsela zida zake. Mofananamo, “wanchito wopanda cifukwa cocitila manyazi” amadziŵa bwino kuseŵenzetsa zida za mu Thuboksi Yathu. (2 Tim. 2:15) Yankhani mafunso otsatilawa kuti muone ngati muzidziŵa bwino zida zathu za mu ulaliki.
MVETSELANI KWA MULUNGU KUTI MUKHALE NDI MOYO WAMUYAYA
Kodi cida cimeneci anacipangila ndani?—mwb17.03 5 ¶1-2
Mungaciseŵenzetse bwanji potsogoza phunzilo la Baibo?—km 7/12 3 ¶6
Ni cida cina citi cimene mungaseŵenzetse pokonzekeletsa wophunzila wanu ubatizo?—km 7/12 3 ¶7
UTHENGA WABWINO WOCOKELA KWA MULUNGU
Kodi cida cimeneci cisiyana bwanji na zida zina zophunzitsila?—km 3/13 4-5 ¶3-5
Kodi tifunika kucita ciani tikagaŵila cida cimeneci?—km 9/15 3 ¶1
Kodi mungaseŵenzetse bwanji cida cimeneci potsogoza phunzilo la Baibo?—mwb16.01 8
Ni Liti pamene tingayambe phunzilo m’buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse?—km 3/13 7 ¶10
ZIMENE BAIBULO INGATIPHUNZITSE
Kodi mfundo zikulu komanso zakumapeto tingaziseŵenzetse bwanji? —mwb16.11 5 ¶2-3
NDANI AMENE AKUCITA CIFUNILO CA YEHOVA MASIKU ANO?
Ni liti pamene tingaseŵenzetse cida cimeneci?—mwb17.03 8 ¶1
Tingaseŵenzetse bwanji cida cimeneci pokambilana na anthu?—mwb17.03 8, bokosi