Nyimbo ya Solomo
2 “Ine ndine duwa wamba lamʼchigwa chamʼmphepete mwa nyanja,
Ndine duwa chabe lamʼchigwa.”+
2 “Mofanana ndi duwa limene lili pakati pa minga,
Ndi mmene alili wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.”
3 “Mofanana ndi mtengo wa maapozi pakati pa mitengo yamʼnkhalango,
Ndi mmene alili wachikondi wanga pakati pa ana aamuna.
Ndikulakalaka kwambiri nditakhala pansi pamthunzi wa wokondedwa wanga.
Ndipo chipatso chake ndi chotsekemera.
4 Iye anandipititsa kunyumba ya phwando,*
Ndipo chikondi chake kwa ine chinali ngati mbendera yozikidwa pambali panga.
5 Ndipatseni mphesa zouma zoumba pamodzi+ kuti zinditsitsimule.
Ndipatseni maapozi kuti ndipeze mphamvu,
Chifukwa chikondi chikundidwalitsa.
6 Dzanja lake lamanzere lili pansi pa mutu wanga,
Ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.+
7 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu,
Pali insa+ ndiponso pali mphoyo zakutchire kuti:
Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.+
8 Ndikumva wachikondi wanga akubwera.
Taonani! Uyo akubwera apoyo,
Akukwera mapiri ndipo akudumpha zitunda.
9 Wachikondi wanga ali ngati insa komanso mphoyo yaingʼono.+
Taonani! Iye waima kuseri kwa khoma la nyumba yathu.
Akuyangʼana mʼmawindo,
Akusuzumira pazotchingira mʼmawindo.
10 Wachikondi wanga wandiuza kuti:
‘Nyamuka wokondedwa wanga,
Ndiwe wokongola kwa ine, tiye tizipita.
11 Taona! Nyengo yamvula yadutsa.
Mvula yatha ndipo yapita.
12 Maluwa ayamba kuoneka mʼdziko,+
Nthawi yodulira mpesa yakwana,+
Ndipo mʼdziko lathu mukumveka kuimba kwa njiwa.+
13 Nkhuyu zoyambirira+ zapsa mumtengo wa mkuyu.
Mpesa wachita maluwa ndipo ukununkhira.
Nyamuka bwera kuno,
Wokondedwa wanga wokongola, tiye tizipita.
14 Iwe njiwa yanga, amene uli mʼmalo obisika apathanthwe,+
Amene uli mʼmingʼalu yamʼmalo otsetsereka,
Ndikufuna ndikuone komanso kumva mawu ako,+
Chifukwa mawu ako ndi osangalatsa ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+
15 “Tigwirireni nkhandwe,
Nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa,
Chifukwa minda yathu ya mpesa yachita maluwa.”
16 “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.+