Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
109 Inu Mulungu amene ndimakutamandani,+ musakhale chete.
2 Chifukwa anthu oipa ndiponso achinyengo akundinenera zinthu zoipa
Iwo akulankhula zinthu zabodza zokhudza ine.+
3 Andizungulira ndipo akulankhula mawu osonyeza kuti amadana nane,
Komanso akundiukira popanda chifukwa.+
4 Ndikawasonyeza chikondi amandiimba mlandu,+
Koma ine ndimapitiriza kupemphera.
6 Muikireni woweruza woipa,
Ndipo kudzanja lake lamanja kuime amene akumuimba mlandu.*
9 Ana ake* akhale amasiye,
Ndipo mkazi wake akhalenso wamasiye.
10 Ana ake* aziyendayenda ndipo akhale opemphapempha.
Azichoka mʼmabwinja mmene akukhala, nʼkukafunafuna chakudya.
11 Wangongole alande* zonse zimene ali nazo,
Ndipo anthu achilendo alande zinthu zake.
12 Pasapezeke womuchitira chifundo,*
Ndipo pasapezeke aliyense wosonyeza kukoma mtima kwa ana ake amasiyewo.
13 Mbadwa zake ziphedwe.+
Dzina lawo lisadzakumbukiridwe mu mʼbadwo wotsatira.
14 Yehova akumbukire zolakwa za makolo ake,+
Ndipo tchimo la mayi ake lisafufutidwe.
15 Nthawi zonse Yehova azikumbukira zimene achita.
Ndipo achititse kuti asadzakumbukiridwenso padziko lapansi.+
16 Chifukwa chakuti sanakumbukire kusonyeza chifundo,*+
Koma anapitiriza kuthamangitsa munthu woponderezedwa,+ wosauka komanso wosweka mtima,
Kuti amuphe.+
17 Iye ankakonda kutemberera, choncho matemberero anabwera pa iye.
Analibe mtima wofuna kudalitsa, choncho sanalandire madalitso.
18 Iye anavekedwa matemberero ngati chovala.
Ndipo anathiridwa mʼthupi mwake ngati madzi,
Ndiponso mʼmafupa ake ngati mafuta.
19 Matemberero ake akhale ngati nsalu imene amadziphimba nayo,+
Komanso ngati lamba amene amavala nthawi zonse.
20 Amenewa ndi malipiro amene Yehova amapereka kwa amene amalimbana nane+
Komanso kwa amene amalankhula zinthu zoipa zokhudza ine.
21 Koma inu, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,
Ndithandizeni kuti dzina lanu lilemekezedwe.+
Ndipulumutseni chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino.+
23 Ine ndikutha ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka.
Ndili ngati dzombe lomwe lakutumulidwa pa chovala.
24 Mawondo anga akunjenjemera chifukwa chosala kudya,
Ndawonda ndipo ndatsala mafupa okhaokha.*
25 Iwo akumandinyoza.+
Akandiona akumapukusa mitu yawo.+
26 Ndithandizeni, inu Yehova Mulungu wanga.
Ndipulumutseni ndi chikondi chanu chokhulupirika.
27 Iwo adziwe kuti zimenezi zachitika chifukwa cha dzanja lanu.
Adziwe kuti inu Yehova mwachita zimenezi.
28 Alekeni anditemberere, koma inu mundipatse madalitso.
Iwo akaimirira kuti andiukire, inu muwachititse manyazi,
Koma lolani ine mtumiki wanu kuti ndisangalale.
30 Pakamwa panga padzatamanda Yehova ndi mtima wonse.
Ndidzamutamanda pamaso pa anthu ambiri.+
31 Chifukwa adzaima kudzanja lamanja la munthu wosauka,
Kuti amupulumutse kwa amene akumuweruza mopanda chilungamo.