Yobu
5 Masiku a munthu ndi odziwika,+
Ndipo chiwerengero cha miyezi yake chili ndi inu.
Mwamuikira lamulo kuti asalipitirire.
6 Siyani kumuyang’anitsitsa kuti apumule,+
Mpaka apeze chisangalalo ngati mmene amachitira waganyu pakutha pa tsiku.
7 Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo.
Ukadulidwa umaphukanso,+
Ndipo nthambi yake idzakhalapo mpaka kalekale.
8 Muzu wake ukakalamba m’nthaka,
Ndipo chitsa chake chikafa m’fumbi,
9 Ukadzangomva fungo la madzi udzaphukira,+
Ndipo udzamera nthambi ngati mtengo watsopano.+
10 Koma mwamuna wamphamvu amafa ndipo amagona pansi atagonjetsedwa.
Munthu wochokera kufumbi amatha. Kodi ali kuti?+
12 Anthu nawonso amagona pansi osadzuka.+
Sadzadzuka mpaka kumwamba kutachoka,+
Sadzadzutsidwa ku tulo tawo.+
14 Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?+
Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza,+
Mpaka mpumulo wanga utafika.+
18 Ngakhale phiri limagwa n’kugumukagumuka,
Ngakhale thanthwe limasunthidwa pamalo ake.
19 Madzi amaperesa ngakhale miyala.
Akamathamanga amakokolola dothi la padziko lapansi.
Inunso mwawononga chiyembekezo cha munthu.
21 Ana ake amalemekezedwa, koma iye sadziwa zimenezo.+
Iwo amakhala opanda pake, koma iye sawaganizira.
22 Mnofu wake umawawa adakali nawo,
Ndipo moyo wake umapitiriza kulira udakali mwa iye.”