Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
134 Tamandani Yehova,+
Inu nonse atumiki a Yehova,+
Inu amene mumaimirira m’nyumba ya Yehova usiku.+
2 Pamene mukupemphera mutakweza manja anu, muzikhala oyera,+
Ndipo tamandani Yehova.+
3 Yehova, amene ndiye Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+
Akudalitseni ali ku Ziyoni.+