Genesis 12:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera.+ Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso* chifukwa cha iwe.”+ Genesis 28:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+ Genesis 31:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu, Mulungu amene Isaki anali kumuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, n’chifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+ Numeri 24:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Iye anagwada pansi. Anagona pansi ngati mkango.Ngati mkango, ndani angayese kum’dzutsa?+Odalitsa iwe n’ngodalitsika,+Ndipo otemberera iwe n’ngotembereredwa.”+ Ezekieli 25:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu walanga nyumba ya Yuda ndipo akupitiriza kuilanga ndi kuichitira zinthu zoipa kwambiri,+
3 Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera.+ Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso* chifukwa cha iwe.”+
3 Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+
42 Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu, Mulungu amene Isaki anali kumuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, n’chifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+
9 Iye anagwada pansi. Anagona pansi ngati mkango.Ngati mkango, ndani angayese kum’dzutsa?+Odalitsa iwe n’ngodalitsika,+Ndipo otemberera iwe n’ngotembereredwa.”+
12 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu walanga nyumba ya Yuda ndipo akupitiriza kuilanga ndi kuichitira zinthu zoipa kwambiri,+