Ekisodo 1:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Koma pamene anali kuwazunza kwambiri m’pamenenso anali kuwonjezeka ndi kufalikira mowirikiza, mwakuti Aiguputo anachita mantha kwambiri ndi ana a Isiraeliwo.+ Ekisodo 23:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+ Deuteronomo 11:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Palibe munthu amene adzaima kuti alimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzapondapo kugwidwa ndi mantha aakulu ndi kukuopani,+ monga mmene anakulonjezerani. Yoswa 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ndipo iye anauza amunawo kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.+ Ife tagwidwa ndi mantha chifukwa cha inu,+ ndipo anthu a dziko lino ataya mtima chifukwa chokuopani.+ Salimo 14:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,+Pakuti Yehova ali pakati pa khamu* la anthu olungama.+
12 Koma pamene anali kuwazunza kwambiri m’pamenenso anali kuwonjezeka ndi kufalikira mowirikiza, mwakuti Aiguputo anachita mantha kwambiri ndi ana a Isiraeliwo.+
27 “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+
25 Palibe munthu amene adzaima kuti alimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzapondapo kugwidwa ndi mantha aakulu ndi kukuopani,+ monga mmene anakulonjezerani.
9 Ndipo iye anauza amunawo kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.+ Ife tagwidwa ndi mantha chifukwa cha inu,+ ndipo anthu a dziko lino ataya mtima chifukwa chokuopani.+