14 Choncho, a m’chigawo cha mafuko atatu cha ana a Yuda ndiwo anayamba kunyamuka m’magulu awo.+ Mtsogoleri wa asilikali awo anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu.
3 Choncho akulu onse+ a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Mfumu Davide anachita nawo pangano+ ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.+