Ekisodo 24:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Kwera m’phiri muno ufike kwa ine ndi kukhala momwe muno, pakuti ndikufuna kukupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+ Ekisodo 32:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kenako, Mose anatembenuka n’kutsika m’phirimo+ atanyamula miyala yosema ya Umboni+ m’manja mwake. Miyalayo inali yolembedwapo mawu mbali zonse ziwiri. Inali yolembedwapo mawu mbali iyi ndi mbali inayo. Deuteronomo 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Pamenepo anakuuzani pangano lake,+ Mawu Khumi,*+ ndipo anakulamulani kuti muzilisunga. Kenako analemba Mawu Khumiwo pamiyala iwiri yosema.+ Deuteronomo 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 “Kenako ndinatembenuka ndi kutsika m’phirimo pamene phirilo linali kuyaka moto,+ ndipo miyala iwiri ya pangano inali m’manja mwanga.+
12 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Kwera m’phiri muno ufike kwa ine ndi kukhala momwe muno, pakuti ndikufuna kukupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+
15 Kenako, Mose anatembenuka n’kutsika m’phirimo+ atanyamula miyala yosema ya Umboni+ m’manja mwake. Miyalayo inali yolembedwapo mawu mbali zonse ziwiri. Inali yolembedwapo mawu mbali iyi ndi mbali inayo.
13 Pamenepo anakuuzani pangano lake,+ Mawu Khumi,*+ ndipo anakulamulani kuti muzilisunga. Kenako analemba Mawu Khumiwo pamiyala iwiri yosema.+
15 “Kenako ndinatembenuka ndi kutsika m’phirimo pamene phirilo linali kuyaka moto,+ ndipo miyala iwiri ya pangano inali m’manja mwanga.+