5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+
18 ‘Yehova ndi wosakwiya msanga,+ ndipo ndi wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Amakhululukira wolakwa ndi wophwanya malamulo,+ koma iye salekerera konse wolakwa osam’langa.+ Amalanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za makolo awo.’+
19 Ndaika moyo ndi imfa, dalitso+ ndi temberero+ pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu.+ Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+