18 “Ukadzatero adzamvera mawu ako.+ Pamenepo, iweyo ndi akulu a Isiraeli mudzapite kwa mfumu ya Iguputo ndi kuiuza kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi+ walankhula nafe.+ Chotero mutilole chonde, tiyende ulendo wamasiku atatu m’chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’+