Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 39:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+

  • Deuteronomo 5:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “‘Usachite chigololo.+

  • Miyambo 6:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru mumtima mwake.+ Amene amachita zimenezi amawononga moyo wake.+

  • Mateyu 5:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’+

  • Mateyu 5:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo+ mumtima mwake.+

  • Aroma 13:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Chifukwa malamulo onena kuti, “Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,+ Usabe,+ Usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+

  • 1 Akorinto 6:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Thawani dama.+ Tchimo lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita dama amachimwira thupi lake.+

  • Aheberi 13:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena