Levitiko 20:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “‘Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake,+ aziphedwa ndithu.+ Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.+ Miyambo 20:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Aliyense wotemberera bambo ake ndi mayi ake,+ nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ Miyambo 30:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pali m’badwo umene umatemberera ngakhale abambo awo ndiponso umene sudalitsa ngakhale amayi awo.+ Miyambo 30:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya. Mateyu 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+
9 “‘Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake,+ aziphedwa ndithu.+ Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.+
17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.
4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+