10 Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo yophimbira machimo,+ panyanga za guwalo kuti aziphimbira machimo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ m’mibadwo yanu yonse. Kwa Yehova, guwalo ndi lopatulika koposa.”
9 Ndipo m’mwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo,+ muziliza lipenga la nyanga ya nkhosa lolira mokwera kwambiri.+ Muziliza lipenga la nyanga ya nkhosalo m’dziko lanu lonse pa tsiku lochita mwambo wophimba machimo.+
7 Komatu, ngati tikuyenda m’kuunika ngati mmene iye alili m’kuunika,+ ndiye kuti ndife ogwirizana,+ ndipo magazi+ a Yesu Mwana wake akutiyeretsa+ ku uchimo wonse.+