-
1 Samueli 12:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ine ndaima pamaso panu. Munditsutse pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa+ wake: Alipo kodi amene ndinam’tengerapo ng’ombe kapena bulu wake?+ Alipo kodi amene ndinam’chitirapo chinyengo, kapena kum’pondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisaone zimene anachita?+ Ndili wokonzeka kukubwezerani anthu inu.”+
-
-
Amosi 5:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Inu mukulamula anthu osauka kuti akulipireni mwa kukupatsani zokolola zawo za m’munda, ndiponso kuti azikhoma msonkho mwa kupereka mbewu za m’munda.+ Choncho chifukwa mwachita zinthu zimenezi, simudzapitiriza kukhala m’nyumba zamiyala yosema zimene mwamanga+ ndipo simudzamwa vinyo wochokera m’minda yanu ya mpesa yosiririkayo.+
-