2 Iwo alakalaka minda ya anthu ena ndipo ailanda.+ Alakalakanso nyumba za anthu ena n’kuzitenga kukhala zawo.+ Atenga mwachinyengo cholowa cha munthu ndi cha banja lake.+
10 n’kunena kuti: “Iwe munthu wodzazidwa ndi mtundu uliwonse wa chinyengo ndi zoipa, mwana wa Mdyerekezi,+ mdani wa chilichonse cholungama, kodi sudzaleka kupotoza njira zowongoka za Yehova?