Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndiyeno azibweretsa kwa Yehova nsembe yake ya kupalamula+ chifukwa cha tchimo limene wachita. Azibweretsa nkhosa yaing’ono yaikazi+ kapena mbuzi yaing’ono yaikazi kuti ikhale nsembe yamachimo. Akatero wansembe aziphimba tchimo la munthuyo.+

  • Levitiko 6:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Monga nsembe yake ya kupalamula, azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema.+ Azipereka kwa wansembe nkhosa ya mtengo wofanana ndi mtengo umene wagamulidwa, kuti ikhale nsembe ya kupalamula.+

  • Levitiko 14:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Kenako wansembeyo azitenga nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi ndi kuipereka monga nsembe ya kupalamula+ pamodzi ndi muyezo umodzi+ wa mafuta uja. Zimenezi aziziweyulira* uku ndi uku monga nsembe yoweyula+ yoperekedwa kwa Yehova.

  • Levitiko 19:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Mwamunayo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe ya kupalamula+ pakhomo la chihema chokumanako.

  • Numeri 6:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Munthuyo ayambirenso masiku ake odzipereka kwa Yehova ngati Mnaziri,+ ndipo abweretse nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi monga nsembe ya kupalamula.+ Masiku oyamba aja sadzawerengedwa chifukwa anaipitsa unaziri wake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena