30 Iye azibweretsa mafuta+ pamodzi ndi nganga monga nsembe kwa Yehova yotentha ndi moto. Azibweretsa mafutawo pamodzi ndi nganga kuti aziweyule* uku ndi uku, monga nsembe yoweyula+ yoperekedwa kwa Yehova.
11 Pamenepo, Aroni auze Aleviwo kuti ayende uku ndi uku pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula*+ ya ana a Isiraeli. Iwo azigwira ntchito yotumikira Yehova.+