25 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yamachimo+ lili motere: Nyama ya nsembe yamachimo iziphedwa pamaso pa Yehova, pamalo+ ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse. Chimenechi ndi chinthu chopatulika koposa.+
13 Ndipo azipha nkhosa yaing’ono yamphongoyo pamalo+ amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza, pamalo oyera.+ Azichita zimenezi chifukwa nsembe ya kupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe ya kupalamula ndi yopatulika koposa.