Levitiko 5:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Munthu akachimwa mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira,+ komabe wapalamula mlandu, pamenepo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+ Numeri 15:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Wansembe apereke nsembe yophimba tchimo la munthuyo, amene walakwira Yehova mosazindikira, kuti akhululukidwe.+ Salimo 119:67 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 67 Ndisanagwe m’masautso ndinali kuchimwa mosadziwa,+Koma tsopano ndimasunga mawu anu.+ Agalatiya 6:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+ Yakobo 2:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Aliyense wosunga Chilamulo akalakwitsa mbali imodzi, walakwira malamulo onse.+
17 “Munthu akachimwa mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira,+ komabe wapalamula mlandu, pamenepo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+
28 Wansembe apereke nsembe yophimba tchimo la munthuyo, amene walakwira Yehova mosazindikira, kuti akhululukidwe.+
6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+