2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli, ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli, wopereka mwana wake aliyense kwa Moleki,*+ aziphedwa ndithu. Nzika za m’dziko lanu zizimupha mwa kum’ponya miyala.
7 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni.
10 Mfumuyo inachititsa kuti ku Tofeti,+ m’chigwa cha ana a Hinomu+ kukhale kosayenera kulambirako, kuti munthu aliyense asawotcheko* mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi pamoto,+ pomupereka kwa Moleki.+