Nehemiya 5:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino ayi.+ Kodi simuyenera kuyenda moopa+ Mulungu+ kuti tipewe chitonzo+ cha adani athu, anthu a mitundu ina?+ Yobu 28:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Ndiyeno anauza munthu kuti,‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+ Miyambo 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa zinthu.+ Nzeru ndi malangizo zimanyozedwa ndi zitsiru.*+ Miyambo 8:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+ 1 Petulo 2:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.+ Kondani gulu lonse la abale,+ opani Mulungu,+ lemekezani mfumu.+
9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino ayi.+ Kodi simuyenera kuyenda moopa+ Mulungu+ kuti tipewe chitonzo+ cha adani athu, anthu a mitundu ina?+
28 Ndiyeno anauza munthu kuti,‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+
13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+
17 Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.+ Kondani gulu lonse la abale,+ opani Mulungu,+ lemekezani mfumu.+