26 Ndiyeno Mose anakaima pachipata cha msasawo, ndipo anati: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwere kwa ine!”+ Ndipo ana onse aamuna a Levi anayamba kusonkhana kwa Mose.
2 Utengenso abale ako a fuko la Levi, amtundu wa bambo ako, kuti azikhala pafupi ndi inu. Azitumikira+ iweyo limodzi ndi ana ako pachihema cha Umboni.+