Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 12:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “‘Tsiku limeneli lidzakhala chikumbutso kwa inu, ndipo muzichitira Yehova chikondwerero m’mibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale, kuti muzichita chikondwerero chimenechi.

  • Levitiko 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 M’mwezi woyamba,* pa tsiku la 14 m’mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la pasika+ wa Yehova.

  • Deuteronomo 16:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Muzisunga mwambo wa m’mwezi wa Abibu*+ pochita chikondwerero cha pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+

  • Ezekieli 45:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “‘M’mwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo, muzichita pasika.+ Muzichita chikondwerero chimenechi kwa masiku 7 ndipo muzidya mikate yopanda chofufumitsa.+

  • Luka 22:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Tsopano tsiku la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa linafika, tsiku loyenera kupha nyama yoperekera nsembe ya pasika.+

  • 1 Akorinto 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano,+ popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu+ waperekedwa+ monga nsembe yathu ya pasika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena