Yoswa 22:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Anawauza kuti: “Bwererani kumahema anu ndi chuma chambiri ndiponso ziweto zambiri, ndi siliva, golide, mkuwa, zitsulo, ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munafunkha+ kwa adani anu n’kugawana ndi abale anu.” 1 Samueli 30:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Ndani angamve zimene mukunenazo? Pakuti gawo limene munthu amene anapita kunkhondo alandire, likhala lofanana ndi gawo limene munthu amene anali kulondera katundu alandire.+ Aliyense alandirapo kenakake.”+ Salimo 68:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Mafumu enieniwo okhala ndi magulu a asilikali amathawa, ndithu amathawadi.+Mkazi wongokhala pakhomo, nayenso amagwira nawo ntchito yofunkha.+
8 Anawauza kuti: “Bwererani kumahema anu ndi chuma chambiri ndiponso ziweto zambiri, ndi siliva, golide, mkuwa, zitsulo, ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munafunkha+ kwa adani anu n’kugawana ndi abale anu.”
24 Ndani angamve zimene mukunenazo? Pakuti gawo limene munthu amene anapita kunkhondo alandire, likhala lofanana ndi gawo limene munthu amene anali kulondera katundu alandire.+ Aliyense alandirapo kenakake.”+
12 Mafumu enieniwo okhala ndi magulu a asilikali amathawa, ndithu amathawadi.+Mkazi wongokhala pakhomo, nayenso amagwira nawo ntchito yofunkha.+