23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anam’berekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+
33 Uwu ndiwo utumiki wa mabanja a ana a Merari,+ monga gawo la utumiki wawo m’chihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni, ndiye aziyang’anira utumiki wawo.”+
8 Ana a Merari anawapatsa ngolo zinayi ndi ng’ombe 8, malinga ndi utumiki wawo+ umene anali kuchita moyang’aniridwa ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.+