Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 17:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Zitatero Mose anauza Yoswa* kuti:+ “Tisankhire amuna, ndipo upite nawo+ kukamenyana ndi Aamaleki. Mawa ndikaima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu woona m’dzanja langa.”+

  • Ekisodo 24:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka, ndipo Mose anakwera m’phiri la Mulungu woona.+

  • Ekisodo 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pamenepo Yehova anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso,+ mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake. Mose akabwerera kumsasa, mtumiki wake+ Yoswa, mwana wa Nuni,+ sanali kuchoka m’chihemacho, popeza anali kalinde.

  • Numeri 27:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chotero Yehova anauza Mose kuti: “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu wolimba mtima,*+ ndipo uike manja ako pa iye.+

  • Deuteronomo 31:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni.+ Iye ndiye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu, ndipo inu mudzaipitikitse.+ Yoswa ndiye adzakutsogolerani ndi kukuwolotsani,+ monga mmene Yehova wanenera.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena