36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune.+ Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzagawira dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+
6 Tsopano ana a Yuda anapita kwa Yoswa ku Giligala.+ Ndipo Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi,+ anauza Yoswa kuti: “Inu mukudziwa bwino za mawu amene Yehova analankhula+ kwa Mose munthu wa Mulungu woona,+ onena za ine ndi inu ku Kadesi-barinea.+