Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+

      “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+

  • Levitiko 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “‘Ngati mukupereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha,+ muzipereka tirigu* wamuwisi wotibula, wokazinga pamoto, kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha.

  • Numeri 18:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+

  • Deuteronomo 26:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 ukatenge zina mwa zipatso zoyambirira+ pa zipatso zonse za m’munda mwako zimene udzakolola m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. Ukaziike m’dengu ndi kupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe kuika dzina lake.+

  • Deuteronomo 26:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Choncho ndabweretsa zipatso zoyambirira mwa zipatso za m’dziko limene Yehova anandipatsa.’+

      “Pamenepo uzikaziika pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kugwada pamaso pa Yehova Mulungu wako.+

  • Nehemiya 10:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Komanso tinafunika kupititsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu,+ zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano+ ndi mafuta+ kwa ansembe kumalo odyera+ m’nyumba ya Mulungu wathu. Tinafunikanso kupititsa chakhumi kwa Alevi+ pa zinthu zochokera m’nthaka yathu, pakuti Aleviwo anali kulandira chakhumi kuchokera m’mizinda yathu yonse ya zaulimi.

  • Miyambo 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena