Ekisodo 23:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+ “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+ Levitiko 23:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mukalowa m’dziko limene ndikukupatsani, n’kukolola mbewu za m’dzikomo, muzibweretsa kwa wansembe mtolo umodzi wa zipatso zanu zoyambirira.+ Numeri 18:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+ 2 Mbiri 31:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ana a Isiraeli+ atangomva mawuwo, anawonjezera zipatso zoyambirira zimene ankapereka za mbewu,+ vinyo watsopano,+ mafuta,+ uchi,+ ndi zokolola zonse zakumunda+ ndipo anabweretsa chakhumi cha zonsezi chochuluka zedi.+ Nehemiya 10:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Tinachita maerewo kuti tipezenso wobweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyamba kucha m’dziko lathu+ chaka ndi chaka, ndi zipatso zoyamba kucha mwa zipatso zonse za mtengo uliwonse.+ Miyambo 3:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+
19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+ “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+
10 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mukalowa m’dziko limene ndikukupatsani, n’kukolola mbewu za m’dzikomo, muzibweretsa kwa wansembe mtolo umodzi wa zipatso zanu zoyambirira.+
12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+
5 Ana a Isiraeli+ atangomva mawuwo, anawonjezera zipatso zoyambirira zimene ankapereka za mbewu,+ vinyo watsopano,+ mafuta,+ uchi,+ ndi zokolola zonse zakumunda+ ndipo anabweretsa chakhumi cha zonsezi chochuluka zedi.+
35 Tinachita maerewo kuti tipezenso wobweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyamba kucha m’dziko lathu+ chaka ndi chaka, ndi zipatso zoyamba kucha mwa zipatso zonse za mtengo uliwonse.+
9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+ ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.+