Levitiko 22:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Ng’ombe kapena nkhosa, musaiphe tsiku limodzi ndi mwana wake.+ Salimo 36:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+ Salimo 145:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Yehova amakomera mtima aliyense,+Ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.+ Miyambo 12:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake,+ koma chisamaliro cha anthu oipa n’chankhanza.+ Mateyu 10:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu?+ Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.+
6 Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+
29 Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu?+ Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.+