Genesis 15:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni,+ ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.+ Genesis 46:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza m’dziko la Kanani.+ Potsirizira pake, Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo. Ekisodo 22:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Musachitire nkhanza mlendo wokhala pakati panu kapena kum’pondereza,+ chifukwa anthu inu munalinso alendo m’dziko la Iguputo.+ Levitiko 19:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa. Muzim’konda mmene mumadzikondera nokha,+ chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Salimo 105:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo,+Yakobo anakhala monga mlendo m’dziko la Hamu.+
13 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni,+ ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.+
6 Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza m’dziko la Kanani.+ Potsirizira pake, Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo.
21 “Musachitire nkhanza mlendo wokhala pakati panu kapena kum’pondereza,+ chifukwa anthu inu munalinso alendo m’dziko la Iguputo.+
34 Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa. Muzim’konda mmene mumadzikondera nokha,+ chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.