23 Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Kwerani ndi kukatenga dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ pamenepo munapandukiranso malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake.+