-
Yoswa 7:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako, ana a Isiraeli anachimwa mwa kuphwanya lamulo lokhudza zinthu zoyenera kuwonongedwa. Anachimwa pamene Akani+ mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatengako zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Chifukwa cha zimenezi, Yehova anakwiya kwambiri ndi ana a Isiraeli.+
-