15 Kwa ana a Isiraeli, kwa mlendo,+ ndi kwa munthu amene wakhaliratu pakati pawo, mizinda 6 imeneyi ikakhala kothawirako aliyense amene wapha munthu mwangozi.+
57 Ana a Aroni anawapatsa mzinda* wothawirako+ wa Heburoni,+ mzinda wa Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Yatiri,+ mzinda wa Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto,