2 Pa nthawi imeneyo m’pamene Solomo anauza akulu a Isiraeli,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a nyumba za makolo+ a ana a Isiraeli kuti asonkhane ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa+ la pangano la Yehova ku+ Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+